Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mika 2:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo akhumbira minda, nailanda; ngakhale nyumba, nazichotsa; asautsa mwamuna ndi nyumba yake, inde munthu ndi cholowa chake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo akhumbira minda, nailanda; ngakhale nyumba, nazichotsa; asautsa mwamuna ndi nyumba yake, inde munthu ndi cholowa chake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Akasirira minda, amailanda. Akakhumbira nyumba, amazilanda. Amavutitsa munthu ndi banja lake, naŵatengera zonse zimene ali nazo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Amasirira minda ndi kuyilanda, amasirira nyumba ndi kuzilanda. Amatenga nyumba ya munthu mwachinyengo, munthu mnzawo kumulanda cholowa chake.

Onani mutuwo Koperani




Mika 2:2
28 Mawu Ofanana  

Ndipo zitatha izi, kunaoneka zotere: Naboti wa ku Yezireele anali ndi munda wampesa, unali mu Yezireelemo, m'mbali mwa nyumba ya Ahabu mfumu ya ku Samariya.


Ndapenyadi dzulo mwazi wa Naboti ndi mwazi wa ana ake, ati Yehova; ndipo ndikubwezera pamunda pano, ati Yehova. Mtengeni tsono, mumponye pamundapo, monga mwa mau a Yehova.


Ngati minda yanga ifuula monditsutsa, ndi nthumbira zake zilira pamodzi;


Usasirire nyumba yake ya mnzako, usasirire mkazi wake wa mnzako, kapena wantchito wake wa mwamuna, kapena wantchito wake wamkazi, kapena ng'ombe yake, kapena bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mnzako.


Yehova adzalowa m'bwalo la milandu ndi okalamba a anthu ake, ndi akulu ake: Ndinu amene mwadya munda wampesa, zofunkha za waumphawi zili m'nyumba zanu;


Tsoka kwa iwo amene aphatikiza nyumba ndi nyumba, amene alumikiza munda ndi munda, kufikira padzapanda malo, ndipo inu mudzasiyidwa nokha pakati padziko!


Koma maso ako ndi mtima wako sizisamalira kanthu koma kusirira, ndi kukhetsa mwazi wosachimwa, ndi kusautsa, ndi zachiwawa, kuti uzichite.


nasautsa osauka ndi osowa, natenga zofunkha, wosabwezera chigwiriro, nakweza maso ake kumafano, nachita chonyansa,


Analandira mphotho mwa iwe kukhetsa mwazi, walandira phindu loonjezerapo, wanyengerera anansi ako ndi kuwazunza, ndipo wandiiwala Ine, ati Ambuye Yehova.


Taona, ndaomba manja pa phindu lako lonyenga waliona, ndi pa mwazi wokhala pakati pako.


Mumatama lupanga lanu, mumachita chonyansa, mumaipsa yense mkazi wa mnansi wake; ndipo kodi mudzakhala nalo dziko cholowa chanu?


Atero Ambuye Yehova, Likufikireni akalonga a Israele inu, lekani kuchita chiwawa, ndi kulanda za eni ake; muchite chiweruzo ndi chilungamo; lekani kupirikitsa anthu anga m'zolowa zao, ati Ambuye Yehova.


Ndipo kalonga asatengeko cholowa cha anthu kuwazunza, ndi kulanda dziko laolao; apatse ana ake cholowa kulemba dziko lakelake, kuti anthu anga asabalalike, yense kuchoka m'dziko lake.


Ndipo anati kwa ine, Wachiona ichi, wobadwa ndi munthu iwe? Chinthu chopepuka ichi kodi ndi nyumba ya Yuda, kuti achite zonyansa azichita kunozi? Pakuti anadzaza dziko ndi chiwawa, nabwereranso kuutsa mkwiyo wanga, ndipo taonani, aika nthambi kumphuno kwao.


ndiwo amene aliralira fumbi lapansi lili pamutu pa wosauka, napotoza njira ya wofatsa; ndipo munthu ndi atate wake amuka kwa namwali yemweyo, kuti aipse dzina langa loyera;


Tamverani mau awa, inu ng'ombe zazikazi za ku Basani, zokhala m'phiri la Samariya, zosautsa aumphawi, zopsinja osowa, zonena kwa ambuyao, Bwerani nacho, timwe.


Tamverani ichi, inu akumeza aumphawi, ndi kuwatha ofatsa m'dziko, ndi kuti,


Tamvanitu ichi, akulu a nyumba ya Yakobo inu, ndi oweruza a nyumba ya Israele inu, akuipidwa nacho chiweruzo, ndi kupotoza zoongoka zonse.


Pakuti anthu ake olemera adzala ndi chiwawa, ndi okhalamo amanena bodza, ndi lilime lao limachita monyenga m'kamwa mwao.


Ndipo ndidzayandikiza kwa inu kuti ndiweruze; ndipo ndidzakhala mboni yakufulumira kutsutsa obwebweta, ndi achigololo, ndi olumbira monama; ndi iwo akunyenga wolembedwa ntchito pa kulipira kwake, akazi amasiye, ndi ana amasiye, ndi wakuipsa mlandu wa mlendo, osandiopa Ine, ati Yehova wa makamu.


Koma tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mutsekera anthu Ufumu wa Kumwamba pamaso pao; pakuti inu nokha simulowamo, ndipo muwaletsa amene alikulowa, kuti asalowemo.


Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pa ndalama; chimene ena pochikhumba, anasochera, nataya chikhulupiriro, nadzipyoza ndi zowawa zambiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa