Mika 2 - Buku LopatulikaMau akutsutsa akulanda za eni 1 Tsoka iwo akulingirira chinyengo, ndi kukonza choipa pakama pao! Kutacha m'mawa achichita, popeza chikhozeka m'manja mwao. 2 Ndipo akhumbira minda, nailanda; ngakhale nyumba, nazichotsa; asautsa mwamuna ndi nyumba yake, inde munthu ndi cholowa chake. 3 Chifukwa chake atero Yehova, Taonani, ndilingirira choipa pa banja ili, chimene simudzachotsako makosi anu, kapena kuyenda modzikuza inu; pakuti nyengo iyi ndi yoipa. 4 Tsiku ilo adzanena fanizo lakunena inu, nadzalira maliro olemerera, ndi kuti, Tapasuka konse; iye asintha gawo la anthu anga; ha! Andichotsera ili! Agawira opikisana minda yathu. 5 Chifukwa chake udzasowa woponya chingwe chamaere m'msonkhano wa Yehova. 6 Musamanenera, amanenera ati. Sadzanenera kwa awa; matonzo sadzachoka. 7 Kodi adzati, Nyumba ya Yakobo iwe, Mzimu wa Yehova waperewera kodi? Izi ndi ntchito zake kodi? Mau anga samchitira zokoma kodi, iye amene ayenda choongoka? 8 Koma ngakhale dzulo anthu anga anauka ngati mdani; mukwatula chofunda kumalaya a iwo opitirira mosatekeseka, ngati anthu osafuna nkhondo. 9 Muwataya akazi a anthu anga kunja kwa nyumba zao zokondweretsa; muchotsa ulemerero wanga kwa ana ao kosatha. 10 Nyamukani, chokani, pakuti popumula panu si pano ai; chifukwa cha udyo wakuononga ndi chionongeko chachikulu. 11 Munthu akayenda ndi mtima wachinyengo ndi kunama, ndi kuti, Ndidzanenera kwa iwe za vinyo ndi chakumwa chakuledzeretsa; iye ndiye mneneri wa anthu ake. 12 Ndidzakumemezani ndithu, Yakobo, inu nonse; ndidzasonkhanitsa ndithu otsala a Israele; ndidzawaika pamodzi ngati nkhosa za ku Bozira; ngati zoweta pakati pa busa pao adzachita phokoso chifukwa cha kuchuluka anthu. 13 Wothyola wakwera pamaso pao; iwo anathyola, napita kuchipata, natuluka pomwepo; ndi mfumu yao yapita pamaso pao, ndipo Yehova awatsogolera. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi