Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 109:31 - Buku Lopatulika

31 Popeza adzaima padzanja lamanja la waumphawi, kumpulumutsa kwa iwo akuweruza koipa moyo wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 Popeza adzaima pa dzanja lamanja la waumphawi, kumpulumutsa kwa iwo akuweruza koipa moyo wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 Paja Chauta amaimirira pafupi ndi munthu wosoŵa, amafuna kumpulumutsa kwa anthu ogamula kuti iyeyo aphedwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 Popeza Iye amayima ku dzanja lamanja la munthu wosowayo, kupulumutsa moyo wake kwa iwo amene agamula molakwa.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 109:31
16 Mawu Ofanana  

Mwapenya; pakuti mumayang'anira chivutitso ndi chisoni kuti achipereke m'manja mwanu; waumphawi adzipereka kwa Inu; wamasiye mumakhala mthandizi wake.


Chifukwa kuti sanakumbukire kuchita chifundo, koma analondola wozunzika ndi waumphawi, ndi wosweka mtima, kuti awaphe.


Ambuye padzanja lamanja lako adzaphwanya mafumu tsiku la mkwiyo wake.


Yehova ndiye wakukusunga; Yehova ndiye mthunzi wako wa kudzanja lako lamanja.


Ndidziwa kuti Yehova adzanenera wozunzika mlandu, ndi kuweruzira aumphawi.


Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse; popeza ali padzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.


Mulungu, mokhala mwake moyera, ndiye Atate wa ana amasiye, ndi woweruza wa akazi amasiye.


Adzaweruza ozunzika a mwa anthu, adzapulumutsa ana aumphawi, nadzaphwanya wosautsa.


Koma ndikhala ndi Inu chikhalire, mwandigwira dzanja langa la manja.


Ukaona anthu alikutsendereza aumphawi, ndi kuchotsa chilungamo ndi chiweruzo mwachiwawa pa dera lina la dziko, usazizwepo; pakuti mkulu wopambana asamalira; ndipo alipo akulu ena oposa amenewo.


Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula; ndipo lilime lonse limene lidzakangana nawe m'chiweruzo udzalitsutsa. Ichi ndi cholowa cha atumiki a Yehova, ndi chilungamo chao chimene chifuma kwa Ine, ati Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa