Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 9:24 - Buku Lopatulika

24 koma wakudzitamandira adzitamandire adzikweze umo, kuti ali wakuzindikira, ndi kundidziwa Ine, kuti ndine Yehova wakuchita zokoma mtima, chiweruziro, ndi chilungamo m'dziko lapansi, pakuti m'menemo ndikondwerera, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 koma wakudzitamandira adzitamandire adzikweze umo, kuti ali wakuzindikira, ndi kundidziwa Ine, kuti ndine Yehova wakuchita zokoma mtima, chiweruziro, ndi chilungamo m'dziko lapansi, pakuti m'menemo ndikondwerera, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Koma ngati wina afuna kunyadira, anyadire ichi chakuti amamvetsa za Ine, ndipo amandidziŵa. Amadziŵa kuti Ine ndine Chauta wokonda chifundo, chilungamo, ndi ungwiro pa dziko lapansi. Ndithudi, pazimenezi ndipo pali mtima wanga.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 koma ngati munthu akufuna kunyadira, anyadire chinthu ichi: kuti iye amamvetsa za Ine ndipo amandidziwa, kuti ndine Yehova, amene ndimakonda chifundo, chilungamo ndiponso ungwiro pa dziko lapansi. Zimenezi ndizo ndimakondwera nazo,” akutero Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 9:24
33 Mawu Ofanana  

Ena atama magaleta, ndi ena akavalo; koma ife tidzatchula dzina la Yehova Mulungu wathu.


Moyo wanga udzatamanda Yehova; ofatsa adzakumva nadzakondwera.


Bukitsani pamodzi ndine ukulu wa Yehova, ndipo tikweze dzina lake pamodzi.


Mwa Mulungu tidzitamanda tsiku lonse, ndipo dzina lanu tidzaliyamika kosatha.


Koma mwatitaya, ndi kutinyazitsa; ndipo simutuluka nao makamu a nkhondo athu.


Mundichitire ine chifundo, Mulungu, monga mwa kukoma mtima kwanu; monga mwa unyinji wa nsoni zanu zokoma mufafanize machimo anga.


Popeza andikondadi ndidzampulumutsa; ndidzamkweza m'mwamba, popeza adziwa dzina langa.


Ndipo mphamvu ya mfumu ikonda chiweruzo; Inu mukhazikitsa zolunjika, muchita chiweruzo ndi chilungamo mu Yakobo.


Ndipo iwo adzakhala ndi mantha ndi manyazi, chifukwa cha Kusi, amene anawatama, ndi Ejipito, amene anawanyadira.


Iwe udzawapeta, ndi mphepo idzawauluza; ndipo kamvulumvulu adzawamwaza; ndipo iwe udzasangalala mwa Yehova, udzadzikuza mwa Woyera wa Israele.


Mwa Yehova mbeu yonse ya Israele idzalungamitsidwa ndi kudzikuza.


Pakuti Ine Yehova ndikonda chiweruziro, ndida chifwamba ndi choipa; ndipo ndidzawapatsa mphotho yao m'zoonadi; ndipo ndidzapangana nao pangano losatha.


Iye anaweruza mlandu wa aumphawi ndi osowa; kumeneko kunali kwabwino. Kodi kumeneko si kundidziwa Ine? Ati Yehova.


Ndipo udzalumbira, Pali Yehova m'zoonadi, m'chiweruziro, ndi m'chilungamo; ndipo mitundu ya anthu idzadzidalitsa mwa Iye, ndipo mwa Iye adzatamandira.


Iye anakuuza, munthuwe, chomwe chili chokoma; ndipo Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.


Ndani Mulungu wofanana ndi Inu, wakukhululukira mphulupulu, wakupitirira zolakwa za otsala a cholowa chake? Sasunga mkwiyo wake kunthawi yonse popeza akondwera nacho chifundo.


Zinthu zonse zinaperekedwa kwa Ine ndi Atate wanga; ndipo palibe munthu adziwa Mwana, koma Atate yekha, ndi palibe wina adziwa Atate, koma Mwana yekha, ndi iye amene Mwana afuna kumuululira.


Zonse zaperekedwa kwa Ine ndi Atate wanga; ndipo palibe munthu azindikira Mwana ali yani, koma Atate; ndipo Atate ali yani, koma Mwana, ndi iye amene Mwana afuna kumuululira Iye.


Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Khristu amene munamtuma.


Ndipo si chotero chokha, koma ife tikondwera ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene talandira naye tsopano chiyanjanitso.


kuti monga mwalembedwa, Iye amene adzitamanda, adzitamande mwa Ambuye.


Koma iye wodzitamandira adzitamandire mwa Ambuye;


Pakuti Mulungu amene anati, Kuunika kudzawala kutuluka mumdima, ndiye amene anawala m'mitima yathu kutipatsa chiwalitsiro cha chidziwitso cha ulemerero wa Mulungu pankhope pa Yesu Khristu.


Koma kudzitamandira ine konsekonse, iai, koma mu mtanda wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene mwa Iye dziko lapansi lapachikidwira ine, ndi ine ndapachikidwira dziko lapansi.


pakuti ife ndife mdulidwe, akutumikira popembedza ndi Mzimu wa Mulungu, nadzitamandira mwa Khristu Yesu, osakhulupirira m'thupi;


Ndipo tidziwa kuti Mwana wa Mulungu wafika, natipatsa ife chidziwitso, kuti tizindikire Woonayo, ndipo tili mwa Woonayo, mwa Mwana wake Yesu Khristu. Iye ndiye Mulungu woona ndi moyo wosatha.


Ndipo Samuele anati, Kodi Yehova akondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zophera, monga ndi kumvera mau a Yehova? Taonani, kumvera ndiko kokoma koposa nsembe, kutchera khutu koposa mafuta a nkhosa zamphongo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa