Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 10:12 - Buku Lopatulika

12 Ukani, Yehova; samulani dzanja lanu, Mulungu; musaiwale ozunzika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ukani, Yehova; samulani dzanja lanu, Mulungu; musaiwale ozunzika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Dzambatukani, Inu Chauta. Onetsani mphamvu zanu, Inu Mulungu. Musaiŵale ozunzika.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Dzukani Yehova! Onetsani dzanja lanu Inu Mulungu. Musayiwale anthu opanda mphamvu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 10:12
15 Mawu Ofanana  

Mudzandiiwala chiiwalire, Yehova, kufikira liti? Mudzandibisira ine nkhope yanu kufikira liti?


Ukani Yehova, Mumtsekereze, mumgwetse, landitsani moyo wanga kwa woipa ndi lupanga lanu;


Onetsani chifundo chanu chodabwitsa, Inu wakupulumutsa okhulupirira Inu kwa iwo akuwaukira ndi dzanja lanu lamanja.


Ukani Yehova; ndipulumutseni, Mulungu wanga! Pakuti mwapanda adani anga onse patsaya; mwawathyola mano oipawo.


Ukani Yehova mu mkwiyo wanu, nyamukani chifukwa cha ukali wa akundisautsa; ndipo mugalamukire ine; mwalamulira chiweruzo.


Musapereke moyo wa njiwa yanu kwa chilombo; musamaiwala moyo wa ozunzika anu nthawi yonse.


Kodi Mulungu waiwala kuchita chifundo? Watsekereza kodi nsoni zokoma zake mumkwiyo?


Pakuti Iye wofuna chamwazi awakumbukira; saiwala kulira kwa ozunzika.


Ndichitireni chifundo, Yehova; penyani kuzunzika kwanga kumene andichitira ondidawo, inu wondinyamula kundichotsa kuzipata za imfa.


Ukani, Yehova, asalimbike munthu; amitundu aweruzidwe pankhope panu.


Nyamukani, Inu woweruza wa dziko lapansi: Bwezerani odzikuza choyenera iwo.


Yehova, dzanja lanu litukulidwa, koma iwo saona; koma iwo adzaona changu chanu cha kwa anthu, nadzakhala ndi manyazi; inde moto udzamaliza adani anu.


Tsopano ndidzauka, ati Yehova; tsopano ndidzanyamuka, tsopano ndidzakwezedwa.


Dzanja lako likwezeke pamwamba pa iwo akuyambana nawe, ndi adani ako onse aonongeke.


Pamenepo Samisoni anaitana kwa Yehova, nati, Yehova, Mulungu, mundikumbukire, ndikupemphani, ndi kundilimbitsa, ndikupemphani, nthawi ino yokha, Mulungu, kuti ndidzilipsiriretu tsopano apa Afilisti, chifukwa cha maso anga awiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa