Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 22:24 - Buku Lopatulika

24 Pakuti sanapeputse ndipo sananyansidwe ndi zunzo la wozunzika; ndipo sanambisire nkhope yake; koma pomfuulira Iye, anamva.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Pakuti sanapeputsa ndipo sananyansidwe ndi zunzo la wozunzika; ndipo sanambisire nkhope yake; koma pomfuulira Iye, anamva.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 “Pakuti sadanyoze munthu wozunzika, sadaipidwe ndi masautso ake, sadamubisire nkhope yake, koma adamumvera pamene adamdandaulira.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Pakuti Iye sanapeputse kapena kunyoza kuvutika kwa wosautsidwayo; Iye sanabise nkhope yake kwa iye. Koma anamvera kulira kwake kofuna thandizo.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 22:24
11 Mawu Ofanana  

M'mene ndinasautsika ndinaitanira pa Yehova; anandiyankha nandiika motakasuka Yehova.


Mulungu wanga, ndiitana usana, koma simuvomereza; ndipo usiku, sindikhala chete.


Koma ine ndine nyongolotsi, si munthu ai, chotonza cha anthu, ndi wonyozedwa ndi anthu.


Munthu uyu wozunzika anafuula, ndipo Yehova anamumva, nampulumutsa m'masautso ake onse.


Mafupa anga onse adzanena, Yehova, afanana ndi Inu ndani, wakulanditsa wozunzika kwa iye amene amposa mphamvu, ndi wozunzika ndi waumphawi kwa iye amfunkhira?


Ndipo musabisire nkhope yanu mtumiki wanu; pakuti ndisautsika ine; mundiyankhe msanga.


Ndipo pamene Yesu anafuula ndi mau aakulu, anati, Atate, m'manja mwanu ndipereka mzimu wanga. Ndipo pakutero anapereka mzimu wake.


Ameneyo, m'masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa