Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 22:23 - Buku Lopatulika

23 Inu akuopa Yehova, mumlemekeze; inu nonse mbumba ya Yakobo, mumchitire ulemu; ndipo muchite mantha ndi Iye, inu nonse mbumba ya Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Inu akuopa Yehova, mumlemekeze; inu nonse mbumba ya Yakobo, mumchitire ulemu; ndipo muchite mantha ndi Iye, inu nonse mbumba ya Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Ndidzati, “Inu omvera Chauta, mtamandeni Iye. Inu nonse ana a Yakobe mlemekezeni Iye, inu nonse ana a Israele, mchitireni Iye ulemu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Inu amene mumaopa Yehova mutamandeni! Inu zidzukulu zonse za Yakobo, mulemekezeni! Muopeni mwaulemu, inu zidzukulu zonse za Israeli!

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 22:23
22 Mawu Ofanana  

Kuti ndione chokomacho cha osankhika anu, kuti ndikondwere nacho chikondwerero cha anthu anu, kuti ndidzitamandire pamodzi ndi cholowa chanu.


Ndidzayamika Yehova kwakukulu pakamwa panga; ndi pakati pa anthu aunyinji ndidzamlemekeza.


Aleluya. Ndidzayamika Yehova ndi mtima wonse, mu upo wa oongoka mtima, ndi mumsonkhano.


Inu akuopa Yehova, khulupirirani Yehova; ndiye mthandizi wao ndi chikopa chao.


Adzadalitsa iwo akuopa Yehova, aang'ono ndi aakulu.


Adzachita chokhumba iwo akumuopa; nadzamva kufuula kwao, nadzawapulumutsa.


Mbumba ya anthu idzamtumikira; kudzanenedwa za Ambuye ku mibadwo yakudza.


Phazi langa liponda pachidikha, m'misonkhano ndidzalemekeza Yehova.


Dziko lonse lapansi liope Yehova, ponse pali anthu achite mantha chifukwa cha Iye.


Ndidzakuyamikani mu msonkhano waukulu; m'chikhamu cha anthu ndidzakulemekezani.


Wopereka nsembe yachiyamiko andilemekeza Ine; ndipo kwa iye wosunga mayendedwe ake ndidzamuonetsa chipulumutso cha Mulungu.


Ndidzakuyamikani, Ambuye, Mulungu wanga, ndi mtima wanga wonse; ndipo ndidzalemekeza dzina lanu nthawi zonse.


Chifukwa chake anthu amphamvu adzakulemekezani Inu, mzinda wa mitundu yakuopsa udzakuopani Inu.


Ndipo chifundo chake chifikira anthu a mibadwomibadwo pa iwo amene amuopa Iye.


Ndipo abusawo anabwera, nalemekeza ndi kutamanda Mulungu pa zinthu zonse anazimva, naziona, monga kunalankhulidwa kwa iwo.


Chifukwa chake mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.


Ndani adzakhala wosaopa ndi wosalemekeza dzina lanu Ambuye? Chifukwa Inu nokha muli woyera; chifukwa mitundu yonse idzadza nidzalambira pamaso panu, popeza zolungama zanu zidaonetsedwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa