Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 11:42 - Buku Lopatulika

42 Koma tsoka inu, Afarisi! Chifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbeu tonunkhira, ndi timbeu tokometsa chakudya ndi ndiwo zonse, ndipo mumaleka chiweruzo ndi chikondi cha Mulungu; mwenzi mutachita izi, ndi kusasiya zinazo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

42 Koma tsoka inu, Afarisi! Chifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbeu tonunkhira, ndi timbeu tokometsa chakudya ndi ndiwo zonse, ndipo mumaleka chiweruzo ndi chikondi cha Mulungu; mwenzi mutachita izi, ndi kusasiya zinazo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

42 “Muli ndi tsoka, inu Afarisi, chifukwa mumapereka chachikhumi cha timbeu tonunkhira, cha timbeu tokometsera chakudya, ndiponso cha mbeu zakudimba za mtundu uliwonse. Koma simulabadako kuchita chilungamo, kapena kukonda Mulungu. Mukadayenera kuchitadi zimenezi, komabe osasiya zinazo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

42 “Tsoka kwa inu Afarisi, chifukwa mumapereka kwa Mulungu chakhumi cha timbewu tonunkhira, ndi timbewu tokometsera chakudya ndi mbewu zina zonse za mʼmunda, koma mumakana chilungamo ndi chikondi cha Mulungu. Mumayenera kuchita zomalizirazi osalekanso kuchita zoyambazi.

Onani mutuwo Koperani




Luka 11:42
22 Mawu Ofanana  

ndi kuti tidzabwera nazo za mtanda wa mkate wathu woyamba, ndi nsembe zathu zokwera, ndi zipatso za mtengo uliwonse, vinyo, ndi mafuta, kwa ansembe, kuzipinda za nyumba ya Mulungu wathu; ndi limodzi la magawo khumi la nthaka yathu kwa Alevi; pakuti Alevi amene amalandira limodzilimodzi la magawo khumi m'midzi yonse yolima ife.


Kuchita chilungamo ndi chiweruzo kupambana ndi nsembe kumkonda Yehova.


Kuli kwabwino kugwira ichi; indetu, usachotsepo dzanja lako pakuti yemwe aopa Mulungu adzatuluka monsemo.


Iye anakuuza, munthuwe, chomwe chili chokoma; ndipo Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.


Mwana alemekeza atate wake, ndi mnyamata mbuye wake; ngati Ine tsono ndine atate, uli kuti ulemu wanga? Ngati Ine ndine mbuye, kundiopa kuli kuti? Ati Yehova wa makamu kwa inu ansembe akupeputsa dzina langa. Ndipo mukuti, Tapeputsa dzina lanu motani?


Mwalemetsa Yehova ndi mau anu. Koma mukuti, Tamlemetsa ndi chiyani? Ndi ichi chakuti munena, Yense wakuchita choipa ali wokoma pamaso pa Mulungu, ndipo akondwera nao; kapena, Ali kuti Mulungu wa chiweruzo?


Kodi munthu adzalanda za Mulungu? Ndipo inu mundilanda Ine. Koma mukuti, Takulandani zotani? Limodzilimodzi la magawo khumi, ndi zopereka.


Koma tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mutsekera anthu Ufumu wa Kumwamba pamaso pao; pakuti inu nokha simulowamo, ndipo muwaletsa amene alikulowa, kuti asalowemo.


Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbeu tonunkhira, ndi katsabola, ndi la chitowe, nimusiya zolemera za chilamulo, ndizo kuweruza kolungama, ndi kuchitira chifundo, ndi chikhulupiriro; koma zijazo munayenera kuzichita, osasiya izi zomwe.


Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mufanafana ndi manda opaka njereza, amene aonekera okoma kunja kwake, koma adzala m'katimo ndi mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zonse.


ndisala chakudya kawiri sabata limodzi; ndipereka limodzi la magawo khumi la zonse ndili nazo.


Koma ndikudziwani inu, kuti mulibe chikondi cha Mulungu mwa inu nokha.


Munthu akati, kuti, Ndikonda Mulungu, nadana naye mbale wake, ali wabodza: pakuti iye wosakonda mbale wake amene wamuona, sangathe kukonda Mulungu amene sanamuone.


Ndipo Samuele anati, Kodi Yehova akondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zophera, monga ndi kumvera mau a Yehova? Taonani, kumvera ndiko kokoma koposa nsembe, kutchera khutu koposa mafuta a nkhosa zamphongo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa