Masalimo 118 - Buku LopatulikaWa Salimo alemekeza Mulungu womlanditsa m'manja mwa adani 1 Yamikani Yehova; pakuti Iye ndiye wabwino; pakuti chifundo chake nchosatha. 2 Anene tsono Israele, kuti chifundo chake nchosatha. 3 Anene tsono nyumba ya Aroni, kuti chifundo chake nchosatha. 4 Anene tsono iwo akuopa Yehova, kuti chifundo chake nchosatha. 5 M'mene ndinasautsika ndinaitanira pa Yehova; anandiyankha nandiika motakasuka Yehova. 6 Yehova ndi wanga; sindidzaopa; adzandichitanji munthu? 7 Yehova ndi wanga, mwa iwo akundithandiza; m'mwemo ndidzaona chofuna ine pa iwo akundida. 8 Kuthawira kwa Yehova nkokoma koposa kukhulupirira munthu. 9 Kuthawira kwa Yehova nkokoma koposa kukhulupirira akulu. 10 Amitundu onse adandizinga, zedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula. 11 Adandizinga, inde, adandizinga: Indedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula. 12 Adandizinga ngati njuchi; anazima ngati moto waminga; indedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula. 13 Kundikankha anandikankha ndikadagwa; koma Yehova anandithandiza. 14 Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga; ndipo anakhala chipulumutso changa. 15 M'mahema a olungama muli liu lakufuula mokondwera Dzanja lamanja la Yehova ndi la chipulumutso: 16 Dzanja lamanja la Yehova likwezeka, Dzanja lamanja la Yehova lichita mwamphamvu. 17 Sindidzafa koma ndidzakhala ndi moyo, ndipo ndidzafotokozera ntchito za Yehova. 18 Kulanga anandilangadi Yehova: koma sanandipereke kuimfa ai. 19 Nditsegulireni zipata za chilungamo; ndidzalowamo, ndidzayamika Yehova. 20 Chipata cha Yehova ndi ichi; olungama adzalowamo. 21 Ndidzakuyamikani, popeza munandiyankha, ndipo munakhala chipulumutso changa. 22 Mwala umene omangawo anaukana wakhala mutu wa pangodya. 23 Ichi chidzera kwa Yehova; nchodabwitsa ichi pamaso pathu. 24 Tsiku ili ndilo adaliika Yehova; tidzasekera ndi kukondwera m'mwemo. 25 Tikupemphani, Yehova, tipulumutseni tsopano; tikupemphani, Yehova, tipindulitseni tsopano. 26 Wodala wakudzayo m'dzina la Yehova; takudalitsani kochokera m'nyumba ya Yehova. 27 Yehova ndiye Mulungu, amene anatiunikira; mangani nsembe ndi zingwe, kunyanga za guwa la nsembe. 28 Inu ndinu Mulungu wanga, ndipo ndidzakuyamikani; ndinu Mulungu wanga, ndidzakukwezani. 29 Yamikani Yehova, pakuti Iye ndiye wabwino, pakuti chifundo chake nchosatha. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi