Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 118:12 - Buku Lopatulika

12 Adandizinga ngati njuchi; anazima ngati moto waminga; indedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Adandizinga ngati njuchi; anazima ngati moto waminga; indedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Adandizinga ngati njuchi, koma adatha msanga ngati moto wapaminga. Ndidaŵaononga ndi mphamvu za dzina la Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Anandizinga ngati njuchi, koma anatha msanga ngati moto wapaminga; mʼdzina la Yehova ndinawawononga.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 118:12
18 Mawu Ofanana  

Koma oipa onse adzakhala ngati minga yoyenera kuitaya, pakuti siigwiridwa ndi dzanja;


Yehova akuvomereze tsiku la nsautso; dzina la Mulungu wa Yakobo likuike pamsanje;


Tidzafuula mokondwera mwa chipulumutso chanu, ndipo m'dzina la Mulungu wathu tidzakweza mbendera; Yehova akwaniritse mapempho ako onse.


Miphika yanu isanagwire moto waminga, adzaiuluza, yaiwisi ndi yoyaka.


Yehova, Ambuye wathu, dzina lanu liposadi nanga padziko lonse lapansi!


Pakuti kuseka kwa chitsiru kunga minga ilikuthetheka pansi pa mphika; ichinso ndi chabe.


Ndilibe ukali; ndani adzalimbanitsa lunguzi ndi minga ndi Ine kunkhondo? Ndiziponde ndizitenthe pamodzi.


Ndipo mitundu ya anthu idzanga potentha miyala yanjeresa; monga minga yodulidwa, nitenthedwa ndi moto.


Pakuti chinkana akunga minga yoyangayanga, naledzera nacho choledzeretsa chao, adzathedwa konse ngati chiputu chouma.


Ndipo Aamori, akukhala m'mapiri muja, anatuluka kukomana ndi inu, nakupirikitsani, monga zimachita njuchi, nakukanthani mu Seiri, kufikira ku Horoma.


Ndipo Davide anati kwa Mfilistiyo, Iwe ukudza kwa ine ndi lupanga, ndi mkondo, ndi nthungo; koma ine ndafika kwa iwe m'dzina la Yehova wa makamu, Mulungu wa ankhondo a Israele amene iwe unawanyoza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa