Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 118:7 - Buku Lopatulika

7 Yehova ndi wanga, mwa iwo akundithandiza; m'mwemo ndidzaona chofuna ine pa iwo akundida.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Yehova ndi wanga, mwa iwo akundithandiza; m'mwemo ndidzaona chofuna ine pa iwo akundida.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Chauta ali pa mbali yanga kuti andithandize. Odana nane ndidzaŵayang'ana monyoza nditaŵapambana.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Yehova ali nane; Iye ndiye thandizo langa. Ndidzayangʼana adani anga mwachipambano.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 118:7
10 Mawu Ofanana  

Pamenepo mzimu unavala Amasai, ndiye wamkulu wa makumi atatuwo, nati iye, Ndife anu, Davide, tivomerezana nanu mwana wa Yese inu: mtendere, mtendere ukhale ndi inu, ndi mtendere ukhale ndi athandizi anu; pakuti Mulungu wanu akuthandizani. Ndipo Davide anawalandira, nawaika akulu a magulu.


Mtima wake ngwochirikizika, sadzachita mantha, kufikira ataona chofuna iye pa iwo omsautsa.


Taonani, Mulungu ndiye mthandizi wanga, Ambuye ndiye wachirikiza moyo wanga.


Ine mwini ndidzapereka nsembe yaufulu kwa Inu, ndidzayamika dzina lanu, Yehova, pakuti nlokoma.


Pakuti anandilanditsa m'nsautso yonse; ndipo ndapenya ndi diso langa icho ndakhumbira pa adani anga.


Anaombola moyo wanga kunkhondo, ndikhale mumtendere, pakuti ndiwo ambiri okangana nane.


Mulungu wa chifundo changa adzandichingamira, adzandionetsa tsoka la adani anga.


Musawapheretu, angaiwale anthu anga, muwabalalitse mwa mphamvu yanu, ndipo muwagwetse, Ambuye, ndinu chikopa chathu.


Diso langa lapenya chokhumba ine pa iwo ondilalira, m'makutu mwanga ndamva chokhumba ine pa iwo akuchita zoipa akundiukira.


Pakuti Ine Yehova Mulungu wako ndidzagwira dzanja lako lamanja, ndi kunena kwa iwe, Usaope ndidzakuthandiza iwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa