Mulungu akuitana ana ake kukhala oyera. Kukhala oyera ndiko kukhala opulidwa, odzipereka kwa Mulungu. Kuti tikhalebe oyera tiyenera kupewa chilichonse chomwe Mulungu sachikonda, ndipo Mawu ake ndiye chitsogozo chathu chabwino kwambiri choti tidziwe zimenezo. Werengani Mawu ake tsiku lililonse ndipo mudzamudziwa bwino Mulungu. Mukatero, mudzadziwa chabwino ndi choipa, chomwe chimakufikitsani pafupi ndi Ambuye komanso chomwe chimakutalikirani.
(Masalimo 119:9) Mnyamata adzayeretse bwanji njira yake? Ndi kusunga mawu anu. Yesu Khristu anapereka moyo wake chifukwa cha ife kuti atiyeretse ndi kutikhala oyera. Ngati mumakondadi Atate wanu wakumwamba, mudzapewa chilichonse chomwe chimakutalikirani kwa Iye. Mudzakhala osamala tsiku lililonse ndipo mudzafune kukhala oyera pa chilichonse chomwe muchita.
Tsiku lililonse muyenera kufunafuna kuyera kumene Mulungu akuitanani kuti mukaone Iye. Mawu ake amati: Fufuzani mtendere ndi onse, ndi chiyero; popanda icho palibe munthu adzaona Ambuye. (Ahebri 12:14) Atate wanu wakumwamba akuyuna kuti mukaonekere pamaso pake muli oyera, kuti muchotse chilichonse chomwe chimadetsa thupi lanu ndi mzimu wanu. Mu gawo lino mupeza mavesi ambiri okhudza kuyera ndi kufunika kwake kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.
Yehova, ndani adzagonera m'chihema mwanu? Adzagonera ndani m'phiri lanu lopatulika? Iye wakuyendayo mokwanira, nachita chilungamo, nanena zoonadi mumtima mwake.
Koma muyambe mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.
Koma iwe, munthu wa Mulungu iwe, thawa izi; nutsate chilungamo, chipembedzo, chikhulupiriro, chikondi, chipiriro, chifatso.
Koma mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbandakucha, kunkabe kuwala kufikira usana woti mbee.
Chotsalira, abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.
Atsitsimutsa moyo wanga; anditsogolera m'mabande a chilungamo, chifukwa cha dzina lake.
Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.
Iye amene ayenda molungama, nanena molunjika; iye amene anyoza phindu lonyenga, nasansa manja ake kusalandira zokometsera milandu, amene atseka makutu ake kusamva za mwazi, natsinzina maso ake kusayang'ana choipa; iye adzakhala pamsanje; malo ake ochinjikiza adzakhala malinga amiyala; chakudya chake chidzapatsidwa kwa iye; madzi ake adzakhala chikhalire.
Pakuti Yehova Mulungu ndiye dzuwa ndi chikopa; Yehova adzapatsa chifundo ndi ulemerero; sadzakaniza chokoma iwo akuyenda angwiro.
ndipo musapereke ziwalo zanu kuuchimo, zikhale zida za chosalungama; koma mudzipereke inu nokha kwa Mulungu, monga amoyo atatuluka mwa akufa, ndi ziwalo zanu kwa Mulungu zikhale zida za chilungamo.
Ukani molungama, ndipo musachimwe; pakuti ena alibe chidziwitso cha Mulungu. Ndilankhula kunyaza inu.
Ameneyo sanadziwe uchimo anamyesera uchimo m'malo mwathu; kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa Iye.
Chifundo ndi choonadi zisakusiye; uzimange pakhosi pako; uzilembe pamtima pako; Usakangane ndi munthu chabe, ngati sanakuchitire choipa. Usachitire nsanje munthu wachiwawa; usasankhe njira yake iliyonse. Pakuti wamphulupulu anyansa Yehova; koma chinsinsi chake chili ndi oongoka. Yehova atemberera za m'nyumba ya woipa; koma adalitsa mokhalamo olungama. Anyozadi akunyoza, koma apatsa akufatsa chisomo. Anzeru adzalandira ulemu cholowa chao; koma opusa adzakweza manyazi. motero udzapeza chisomo ndi nzeru yabwino, pamaso pa Mulungu ndi anthu.
Ngati mudziwa kuti ali wolungama, muzindikira kuti aliyensenso wakuchita chilungamo abadwa kuchokera mwa Iye.
Mverani Ine, inu amene mudziwa chilungamo, anthu amene mumtima mwao muli lamulo langa; musaope chitonzo cha anthu, ngakhale kuopsedwa ndi kutukwana kwao.
Pakuti Yehova ndiye wolungama; akonda zolungama; woongoka mtima adzapenya nkhope yake.
ndicho chilungamo cha Mulungu chimene chichokera mwa chikhulupiriro cha pa Yesu Khristu kwa onse amene akhulupirira; pakuti palibe kusiyana;
Chifukwa chake khalani akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa; kuyesera chokondweretsa Ambuye nchiyani; ndipo musayanjane nazo ntchito za mdima zosabala kanthu, koma makamakanso muzitsutse; pakuti zochitidwa nao m'tseri, kungakhale kuzinena kuchititsa manyazi. Koma zinthu zonse potsutsika ndi kuunika, zionekera; pakuti chonse chakuonetsa chili kuunika. Mwa ichi anena, Khala maso wogona iwe, nuuke kwa akufa, ndipo Khristu adzawala pa iwe. Potero, penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru; akuchita machawi, popeza masiku ali oipa. Chifukwa chake musakhale opusa, koma dziwitsani chifuniro cha Ambuye nchiyani. Ndipo musaledzere naye vinyo, m'mene muli chitayiko; komatu mudzale naye Mzimu, ndi kudzilankhulira nokha ndi masalimo, ndi mayamiko, ndi nyimbo zauzimu, kuimbira ndi kuimba m'malimba Ambuye mumtima mwanu; ndipo yendani m'chikondi monganso Khristu anakukondani inu, nadzipereka yekha m'malo mwathu, chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale fungo lonunkhira bwino.
Siyana nacho choipa, nuchite chokoma, nukhale nthawi zonse. Pakuti Yehova akonda chiweruzo, ndipo sataya okondedwa ake. Asungika kosatha, koma adzadula mbumba za oipa.
ndi kutiphunzitsa ife kuti, pokana chisapembedzo ndi zilakolako za dziko lapansi, tikhale ndi moyo m'dziko lino odziletsa, ndi olungama, ndi opembedza;
Iye anakuuza, munthuwe, chomwe chili chokoma; ndipo Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.
Kuunika kutulukira oongoka mtima mumdima; Iye ndiye wachisomo, ndi wansoni ndi wolungama.
Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu;
Tiana, munthu asasokeretse inu; iye wakuchita cholungama ali wolungama, monga Iyeyu ali wolungama:
kuchita chikondwero chanu kundikonda, Mulungu wanga; ndipo malamulo anu ali m'kati mwamtima mwanga.
kuti mukakhale osalakwa ndi oona, ana a Mulungu opanda chilema pakati pa mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka, mwa iwo amene muonekera monga mauniko m'dziko lapansi,
kuti muvule, kunena za makhalidwe anu oyamba, munthu wakale, wovunda potsata zilakolako za chinyengo; koma kuti mukonzeke, mukhale atsopano mu mzimu wa mtima wanu, nimuvale munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m'chilungamo, ndi m'chiyero cha choonadi.
Koma thawa zilakolako za unyamata, nutsate chilungamo, chikhulupiriro, chikondi, mtendere, pamodzi ndi iwo akuitana pa Ambuye ndi mitima yoyera.
Iye asungira oongoka mtima nzeru yeniyeni; ndiye chikopa cha oyenda molunjika; kuti atchinjirize njira za chiweruzo, nadikire khwalala la opatulidwa ake.
Yang'anirani kuti musachite zolungama zanu pamaso pa anthu kuti muonekere kwa iwo; pakuti ngati mutero mulibe mphotho ndi Atate wanu wa Kumwamba.
Pereka njira yako kwa Yehova; khulupiriranso Iye, adzachichita. Ndipo adzaonetsa chilungamo chako monga kuunika, ndi kuweruza kwako monga usana.
Ndidzakondwa kwambiri mwa Yehova, moyo wanga udzakondwerera mwa Mulungu wanga; pakuti Iye wandiveka ine ndi zovala za chipulumutso, nandifunda chofunda cha chilungamo, monga mkwati avala nduwira, ndi monga mkwatibwi adzikometsa yekha ndi miyala yamtengo.
Tiyendeyende koyenera, monga usana; si m'madyerero ndi kuledzera ai, si m'chigololo ndi chonyansa ai, si mu ndeu ndi nkhwidzi ai. Koma valani inu Ambuye Yesu Khristu, ndipo musaganizire za thupi kuchita zofuna zake.
Chifukwa chake chilimikani, mutadzimangira m'chuuno mwanu ndi choonadi, mutavalanso chapachifuwa cha chilungamo;
Komatu ngatinso mukumva zowawa chifukwa cha chilungamo, odala inu; ndipo musaope pakuwaopa iwo, kapena musadere nkhawa;
Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m'chilungamo: kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.
Koma kwa Iye muli inu mwa Khristu Yesu, amene anayesedwa kwa ife nzeru ya kwa Mulungu, ndi chilungamo ndi chiyeretso ndi chiombolo;
Yehova, munditsogolere m'chilungamo chanu, chifukwa cha akundizondawo; mulungamitse njira yanu pamaso panga.
Koma tsopano, pamene munamasulidwa kuuchimo, ndi kukhala akapolo a Mulungu, muli nacho chobala chanu chakufikira chiyeretso, ndi chimaliziro chake moyo wosatha.
Musakhale omangidwa m'goli ndi osakhulupirira osiyana; pakuti chilungamo chigawana bwanji ndi chosalungama? Kapena kuunika kuyanjana bwanji ndi mdima?
kuti choikika chake cha chilamulo chikakwaniridwe mwa ife, amene sitiyendayenda monga mwa thupi, koma monga mwa mzimu.
koma ngati tiyenda m'kuunika, monga Iye ali m'kuunika, tiyanjana wina ndi mnzake, ndipo mwazi wa Yesu Mwana wake utisambitsa kutichotsera uchimo wonse.
pakuti kale munali mdima, koma tsopano muli kuunika mwa Ambuye; yendani monga ana a kuunika, pakuti chipatso cha kuunika tichipeza mu ubwino wonse, ndi chilungamo, ndi choonadi,
Koma wolungama wangayo adzakhala ndi moyo wochokera m'chikhulupiriro: Ndipo ngati abwerera, moyo wanga ulibe kukondwera mwa iye.
koma Yehova wa makamu wakwezedwa m'chiweruziro, ndipo Mulungu Woyera wayeretsedwa m'chilungamo.
Popeza tsono tayesedwa olungama ndi chikhulupiriro, tikhala ndi mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu;
Yehova adziwa masiku a anthu angwiro; ndipo cholowa chao chidzakhala chosatha. Sadzachita manyazi m'nyengo yoipa, ndipo m'masiku a njala adzakhuta.
Maso anga ayang'ana okhulupirika m'dziko, kuti akhale ndi Ine; iye amene ayenda m'njira yangwiro, iyeyu adzanditumikira Ine.
Tiana tanga, izi ndikulemberani, kuti musachimwe. Ndipo akachimwa wina, Nkhoswe tili naye kwa Atate, ndiye Yesu Khristu wolungama;
Si yense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wakuchitayo chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba.
Pomwepo kuunika kwako kudzawalitsa monga m'mawa, ndi kuchira kwako kudzaonekera msangamsanga; ndipo chilungamo chako chidzakutsogolera; ulemerero wa Yehova udzakhala wotchinjiriza pambuyo pako.
Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.
Chomwecho muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.
Chilango chilichonse, pakuchitika, sichimveka chokondweretsa, komatu chowawa; koma chitatha, chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo.
Yehova anandibwezera monga mwa chilungamo changa; anandisudzula monga mwa kusisira kwa manja anga.
Ndikudandaulirani inu tsono, ine wandende mwa Ambuye, muyende koyenera maitanidwe amene munaitanidwa nao,
amene anasenza machimo athu mwini yekha m'thupi mwake pamtanda, kuti ife, titafa kumachimo, tikakhale ndi moyo kutsata chilungamo; ameneyo mikwingwirima yake munachiritsidwa nayo.
M'chilungamo iwe udzakhazikitsidwa, udzakhala kutali ndi chipsinjo, pakuti sudzaopa; udzakhala kutali ndi mantha, pakuti sadzafika chifupi ndi iwe.
Waumphawi woyenda mwangwiro apambana ndi yemwe akhotetsa njira zake, angakhale alemera.
Ndalama zake sakongoletsa mofuna phindu lalikulu, ndipo salandira chokometsera mlandu kutsutsa wosachimwa. Munthu wakuchita izi sadzagwedezeka kunthawi zonse.
Perekani kwa anthu onse mangawa ao; msonkho kwa eni ake a msonkho; kulipira kwa eni ake a kulipidwa; kuopa kwa eni ake a kuwaopa; ulemu kwa eni ake a ulemu.
Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima;
odzala nacho chipatso cha chilungamo, chimene chili mwa Yesu Khristu, kuchitira Mulungu ulemerero ndi chiyamiko.
koma mumpatulikitse Ambuye Khristu m'mitima yanu; okonzeka nthawi zonse kuchita chodzikanira pa yense wakukufunsani chifukwa cha chiyembekezo chili mwa inu, komatu ndi chifatso ndi mantha;
Chifukwa chake muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukulu m'machitidwe ake.
M'menemo aoneka ana a Mulungu, ndi ana a mdierekezi: yense wosachita chilungamo siali wochokera mwa Mulungu; ndi iye wosakonda mbale wake.
Ndipo mwa ichi chomwe, pakutengeraponso changu chonse, muonjezerapo ukoma pa chikhulupiriro chanu, ndi paukoma chizindikiritso; ndi pachizindikiritso chodziletsa; ndi pachodziletsa chipiriro; ndi pachipiriro chipembedzo; ndi pachipembedzo chikondi cha pa abale; ndi pachikondi cha pa abale chikondi.
Sambani, dziyeretseni; chotsani machitidwe anu oipa pamaso panga; lekani kuchita zoipa; phunzirani kuchita zabwino; funani chiweruzo; thandizani osautsidwa, weruzirani ana amasiye, munenere akazi amasiye.
Ndipo anthu athu aphunzirenso asunge ntchito zabwino zofunika, kuti asakhale osabala zipatso.
Wolungama adzaphuka ngati mgwalangwa; adzakula ngati mkungudza wa ku Lebanoni. Iwo ookedwa m'nyumba ya Yehova, adzaphuka m'mabwalo a Mulungu wathu.
kuti mukayenda koyenera Ambuye kukamkondweretsa monsemo, ndi kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino, ndi kukula m'chizindikiritso cha Mulungu;
Mau a m'kamwa mwanga ndi maganizo a m'mtima wanga avomerezeke pamaso panu, Yehova, thanthwe langa, ndi Mombolo wanga.
Limba nayo nkhondo yabwino ya chikhulupiriro, gwira moyo wosatha, umene adakuitanira, ndipo wavomereza chivomerezo chabwino pamaso pa mboni zambiri.
Pakuti Mwana wa Munthu adzabwera mu ulemerero wa Atate wake, pamodzi ndi angelo ake; ndipo pomwepo Iye adzabwezera kwa anthu onse monga machitidwe ao.
koma wopanda chikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna Iye.
Mbuye wake anati kwa iye, Chabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika; unali wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; lowa iwe m'chikondwerero cha mbuye wako.
Mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate ndiwo: kucheza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m'chisautso chao, ndi kudzisungira mwini wosachitidwa mawanga ndi dziko lapansi.
amene adzabwezera munthu aliyense kolingana ndi ntchito zake; kwa iwo amene afunafuna ulemerero ndi ulemu ndi chisaonongeko, mwa kupirira pa ntchito zabwino, adzabwezera moyo wosatha;
Pakuti ife ndife chipango chake, olengedwa mwa Khristu Yesu, kuchita ntchito zabwino, zimene Mulungu anazipangiratu, kuti tikayende m'menemo.
ndipo chimene chilichonse tipempha, tilandira kwa Iye, chifukwa tisunga malamulo ake, ndipo tichita zomkondweretsa pamaso pake.
Munthu wabwino atulutsa zabwino m'chuma chokoma cha mtima wake; ndi munthu woipa atulutsa zoipa m'choipa chake: pakuti m'kamwa mwake mungolankhula mwa kuchuluka kwa mtima wake.
Funani Yehova popezeka Iye, itanani Iye pamene ali pafupi; woipa asiye njira yake, ndi munthu wosalungama asiye maganizo ake, nabwere kwa Yehova; ndipo Yehova adzamchitira chifundo; ndi kwa Mulungu wathu, pakuti Iye adzakhululukira koposa.
Pakuti chipata chili chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali owerengeka.
Pakuti ife tonse tiyenera kuonetsedwa kumpando wakuweruza wa Khristu, kuti yense alandire zochitika m'thupi, monga momwe anachita, kapena chabwino kapena choipa.
Iye ndiye wakukonda chilungamo ndi chiweruzo, dziko lapansi ladzala ndi chifundo cha Yehova.
Chifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero; pakuti icho ndicho chilamulo ndi aneneri.
Woyera m'manja, ndi woona m'mtima, ndiye; iye amene sanakweze moyo wake kutsata zachabe, ndipo salumbira monyenga. Iye adzalandira dalitso kwa Yehova, ndi chilungamo kwa Mulungu wa chipulumutso chake.
Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.
Nditsegulireni zipata za chilungamo; ndidzalowamo, ndidzayamika Yehova. Anene tsono Israele, kuti chifundo chake nchosatha. Chipata cha Yehova ndi ichi; olungama adzalowamo.
Potero, penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru; akuchita machawi, popeza masiku ali oipa.
Chifukwa chake fetsani ziwalozo zili padziko; dama, chidetso, chifunitso chamanyazi, chilakolako choipa, ndi chisiriro, chimene chili kupembedza mafano;
Uchite changu kudzionetsera kwa Mulungu wovomerezeka, wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nao bwino mau a choonadi.
Yembekeza Yehova, nusunge njira yake, ndipo Iye adzakukweza kuti ulandire dziko. Pakudulidwa oipa udzapenya.
ndipo tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino,
Ilipo njira yooneka kwa mwamuna ngati yoongoka; koma matsiriziro ake ndi njira za imfa.