Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Akorinto 15:34 - Buku Lopatulika

34 Ukani molungama, ndipo musachimwe; pakuti ena alibe chidziwitso cha Mulungu. Ndilankhula kunyaza inu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

34 Ukani molungama, ndipo musachimwe; pakuti ena alibe chidziwitso cha Mulungu. Ndilankhula kunyaza inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

34 Mudzidzimuke mumtima mwanu, ndipo muleke kuchimwa. Ena mwa inu sadziŵa Mulungu konse. Ndikukuuzani zimenezi kuti muchite manyazi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

34 Ganizani bwino monga kuyenerera, ndiye lekani kuchimwa; pakuti pali ena amene sadziwa Mulungu. Ndikunena izi kuti muchite manyazi.

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 15:34
17 Mawu Ofanana  

Ndinawabisa mau anu mumtima mwanga, kuti ndisalakwire Inu.


Chitani chinthenthe, ndipo musachimwe. Nenani mumtima mwanu pakama panu, ndipo mukhale chete.


Ndipo apinda lilime lao ngati uta wao, liname; koma akula mphamvu m'dzikomo, koma si pachoonadi; pakuti alinkunkabe nachita zoipa, ndipo sandidziwa Ine, ati Yehova.


Galamukani, oledzera inu, nimulire; bumani, nonse akumwa vinyo, chifukwa cha vinyo watsopano; pakuti waletsedwa pakamwa panu.


Ndipo mwini chombo anadza kwa iye, nanena naye, Utani iwe wam'tulo? Uka, itana Mulungu wako, kapena Mulunguyo adzatikumbukira tingatayike.


Koma Yesu anayankha, nati kwa iwo, Mungolakwa osadziwa malembo, kapena mphamvu za Mulungu.


Zitapita izi Yesu anampeza mu Kachisi, nati kwa iye, Taona, wachiritsidwa; usachimwenso, kuti chingakugwere choipa choposa.


Koma iye anati, Palibe, Ambuye. Ndipo Yesu anati, Inenso sindikutsutsa iwe; pita; kuyambira tsopano usachimwenso.


Muchiyesa chinthu chosakhulupirika, chakuti Mulungu aukitsa akufa?


Ndipo monga iwo anakana kukhala naye Mulungu m'chidziwitso chao, anawapereka Mulungu kumtima wokanika, kukachita zinthu zosayenera;


Ndipo chitani ichi, podziwa inu nyengo, kuti tsopano ndiyo nthawi yabwino yakuuka kutulo; pakuti tsopano chipulumutso chathu chili pafupi koposa pamene tinayamba kukhulupirira.


Sindilembera izi kukuchititsani manyazi, koma kuchenjeza inu monga ana anga okondedwa.


Ndinena ichi kukuchititsani inu manyazi. Kodi nkutero kuti mwa inu palibe mmodzi wanzeru, amene adzakhoza kuweruza pa abale,


Komatu chidziwitso sichili mwa onse; koma ena, ozolowera fano kufikira tsopano, adyako monga yoperekedwa nsembe kwa fano; ndipo chikumbumtima chao, popeza nchofooka, chidetsedwa.


Mwa ichi anena, Khala maso wogona iwe, nuuke kwa akufa, ndipo Khristu adzawala pa iwe.


kosati m'chisiriro cha chilakolako chonyansa, monganso amitundu osadziwa Mulungu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa