Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 101:6 - Buku Lopatulika

6 Maso anga ayang'ana okhulupirika m'dziko, kuti akhale ndi Ine; iye amene ayenda m'njira yangwiro, iyeyu adzanditumikira Ine.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Maso anga ayang'ana okhulupirika m'dziko, kuti akhale ndi Ine; iye amene ayenda m'njira yangwiro, iyeyu adzanditumikira Ine.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Koma anthu okhulupirika am'dziko, ndidzaŵayang'ana moŵakomera mtima, ndipo adzakhala ndi ine. Oyenda m'njira yopanda cholakwa adzanditumikira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Maso anga adzakhala pa okhulupirika mʼdziko, kuti akhale pamodzi ndi ine; iye amene mayendedwe ake ndi wosalakwa adzanditumikira.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 101:6
16 Mawu Ofanana  

Ine ndine wakuyanjana nao onse akukuopani, ndi iwo akusamalira malangizo anu.


M'maso mwake munthu woonongeka anyozeka; koma awachitira ulemu akuopa Yehova. Atalumbira kwa tsoka lake, sasintha ai.


Maso a Yehova ali pa olungama mtima, ndipo makutu ake atchereza kulira kwao.


Pouka oipa anthu amabisala; koma pakufa amenewo olungama achuluka.


Pochuluka olungama anthu akondwa; koma polamulira woipa anthu ausa moyo.


natenge miyala ina, naikhazike m'malo mwa miyala ija; natenge dothi lina, namatenso nyumbayo.


Ndani kodi ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake anamkhazika woyang'anira banja lake, kuwapatsa zakudya pa nthawi yake?


Ngati wina anditumikira Ine, anditsate; ndipo kumene kuli Ine, komwekonso kudzakhala mtumiki wanga. Ngati wina anditumikira Ine, Atate adzamchitira ulemu iyeyu.


Ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa Ine ndekha; kuti kumene kuli Ineko, mukakhale inunso.


Atate, amene mwandipatsa Ine, ndifuna kuti, kumene ndili Ine, iwonso akhale pamodzi ndi Ine; kuti ayang'anire ulemerero wanga, umene mwandipatsa Ine; pakuti munandikonda Ine lisanakhazikike dziko lapansi.


Ndipo ndinamva mau aakulu ochokera ku mpando wachifumu, ndi kunena Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nao, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nao, Mulungu wao;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa