Masalimo 101 - Buku LopatulikaDavide akuti adzasamala okhulupirika nadzachotsa oipa Salimo la Davide. 1 Ndidzaimba zachifundo ndi chiweruzo; ndidzaimba zakukulemekezani Inu, Yehova. 2 Ndidzachita mwanzeru m'njira yangwiro; mudzandidzera liti? Ndidzayenda m'nyumba mwanu ndi mtima wangwiro. 3 Sindidzaika chinthu choipa pamaso panga; chochita iwo akupatuka padera chindiipira; sichidzandimamatira. 4 Mtima wopulukira udzandichokera; sindidzadziwana naye woipa. 5 Wakuneneza mnzake m'tseri ndidzamdula; wa maso odzikuza ndi mtima wodzitama sindidzamlola. 6 Maso anga ayang'ana okhulupirika m'dziko, kuti akhale ndi Ine; iye amene ayenda m'njira yangwiro, iyeyu adzanditumikira Ine. 7 Wakuchita chinyengo sadzakhala m'kati mwa nyumba yanga; wakunena mabodza sadzakhazikika pamaso panga. 8 Mamawa onse ndidzadula oipa onse a m'dziko; kuduliratu onse akuchita zopanda pake kumzinda wa Yehova. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi