Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 101:5 - Buku Lopatulika

5 Wakuneneza mnzake m'tseri ndidzamdula; wa maso odzikuza ndi mtima wodzitama sindidzamlola.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Wakuneneza mnzake m'tseri ndidzamdula; wa maso odzikuza ndi mtima wodzitama sindidzamlola.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Munthu wosinjirira mnzake kuseri ndidzamcheteketsa. Wooneka wonyada ndi wodzikuza sindidzamulekerera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Aliyense wosinjirira mnansi wake mseri ameneyo ndidzamuletsa; aliyense amene ali ndi maso amwano ndi mtima wodzikuza, ameneyo sindidzamulekerera.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 101:5
25 Mawu Ofanana  

Angakhale Yehova ngwokwezeka, apenyanso wopepukayo; koma wodzikuza amdziwira kutali.


Amene sasinjirira ndi lilime lake, nachitira mnzake choipa, ndipo satola miseche pa mnansi wake.


Pakuti Inu muwapulumutsa anthu aumphawi; koma maso okweza muwatsitsa.


Ukhala, nuneneza mbale wako; usinjirira mwana wa mai wako.


Usamnamizire mnzako.


Usatola mbiri yopanda pake; usathandizana naye woipa ndi kukhala mboni yochititsa chiwawa.


Wobisa udani ali ndi milomo yonama; wonena ugogodi ndiye chitsiru.


Kazitape woyendayenda awanditsa zinsinsi; usadudukire woyasama milomo yake.


Maso akunyada, ndi mtima wodzikuza, ndi nyali ya oipa, zili tchimo.


Mphepo ya kumpoto ifikitsa mvula; chomwecho lilime losinjirira likwiyitsa nkhope.


Pali mbadwo wokwezatu maso ao, zikope zao ndi kutukula.


Maso a munthu akuyang'anira kumwamba adzatsitsidwa, ndi kudzikweza kwa anthu kudzaweramitsidwa pansi; ndipo Yehova yekha adzakwezedwa tsiku limenelo.


Anthu oneneza anali mwa iwe, kuti akhetse mwazi; ndipo anadya pamapiri mwa iwe, pakati pa iwe anachita zamanyazi.


Tsono ine Nebukadinezara ndiyamika, ndi kukuza, ndi kulemekeza Mfumu ya Kumwamba, pakuti ntchito zake zonse nzoona, ndi njira zake chiweruzo; ndi oyenda m'kudzikuza kwao, Iye akhoza kuwachepetsa.


Usamayendayenda nusinjirira mwa anthu a mtundu wako; usamatsata mwazi wa mnansi wako; Ine ndine Yehova.


Ndinena ndi inu, anatsikira kunyumba kwake woyesedwa wolungama uyutu, wosati uja ai; pakuti yense wakudzikuza yekha adzachepetsedwa; koma wodzichepetsa yekha adzakulitsidwa.


koma tsopano ndalembera inu kuti musayanjane naye, ngati wina wotchedwa mbale ali wachigololo, kapena wosirira, kapena wopembedza mafano, kapena wolalatira, kapena woledzera, kapena wolanda, kungakhale kukadya naye wotere, iai.


Momwemonso akazi akhale olemekezeka, osadierekeza, odzisunga, okhulupirika m'zonse.


Momwemonso akazi okalamba akhale nao makhalidwe oyenera anthu oyera, osadierekeza, osakodwa nacho chikondi cha pavinyo, akuphunzitsa zokoma;


Musalankhulenso modzikuza kwambiri motero; m'kamwa mwanu musatuluke zolulutsa; chifukwa Yehova ndi Mulungu wanzeru, ndipo Iye ayesa zochita anthu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa