Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 101:1 - Buku Lopatulika

1 Ndidzaimba zachifundo ndi chiweruzo; ndidzaimba zakukulemekezani Inu, Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndidzaimba zachifundo ndi chiweruzo; ndidzaimba zakukulemekezani Inu, Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Ndidzaimba nyimbo zotamanda kukhulupirika ndi kulungama. Ndidzakuimbirani Inu Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Ndidzayimba za chikondi ndi chiweruzo chanu cholungama; kwa Inu Yehova ndidzayimba matamando.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 101:1
14 Mawu Ofanana  

Adzabukitsa chikumbukiro cha ubwino wanu waukulu, nadzaimbira chilungamo chanu.


Mundilanditse kumlandu wa mwazi, Mulungu, ndinu Mulungu wa chipulumutso changa; lilime langa lidzakweza nyimbo ya chilungamo chanu.


Ndidzaimbira zachifundo za Yehova nthawi yonse, pakamwa panga ndidzadziwitsira chikhulupiriko chanu ku mibadwomibadwo.


Kuonetsera chifundo chanu mamawa, ndi chikhulupiriko chanu usiku uliwonse.


Ziyoni anamva nakondwera, nasekerera ana aakazi a Yuda; chifukwa cha maweruzo anu, Yehova.


Iye anakuuza, munthuwe, chomwe chili chokoma; ndipo Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.


Chifukwa chake onani kukoma mtima ndi kuuma mtima kwake kwa Mulungu: kwa iwo adagwa, kuuma kwake; koma kwa iwe kukoma mtima kwake kwa Mulungu, ngati ukhala chikhalire m'kukoma mtimamo; koma ngati sutero, adzakusadza iwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa