Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 34:15 - Buku Lopatulika

15 Maso a Yehova ali pa olungama mtima, ndipo makutu ake atchereza kulira kwao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Maso a Yehova ali pa olungama mtima, ndipo makutu ake atchereza kulira kwao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Ngati mumvera Chauta, adzakuyang'anirani ndipo adzayankha kupempha kwanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Maso a Yehova ali pa olungama ndipo makutu ake ali tcheru kumva kulira kwawo;

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 34:15
12 Mawu Ofanana  

Tsopano Mulungu wanga, maso anu akhale chipenyere, ndi makutu anu chimvere, pemphero lochitika pamalo pano.


Sawachotsera wolungama maso ake, koma pamodzi ndi mafumu pa mpando wao awakhazika chikhazikire, ndipo akwezeka.


Ambuye, imvani liu langa; makutu anu akhale chimverere mau a kupemba kwanga.


Taonani, diso la Yehova lili pa iwo akumuopa Iye, pa iwo akuyembekeza chifundo chake.


Iwowo anaitana, ndipo Yehova anawamva, nawalanditsa kumasautso ao onse.


Munthu uyu wozunzika anafuula, ndipo Yehova anamumva, nampulumutsa m'masautso ake onse.


Siyana nacho choipa, nuchite chokoma, nukhale nthawi zonse.


Izi ndizo muzichite: Nenani choonadi yense ndi mnzake; weruzani zoona ndi chiweruzo cha mtendere m'zipata zanu;


Atero Yehova wa makamu: Kusala kwa mwezi wachinai, ndi kusala kwa mwezi wachisanu, ndi kusala kwa mwezi wachisanu ndi chiwiri, ndi kusala kwa mwezi wakhumi kukhale kwa nyumba ya Yuda chimwemwe ndi chikondwerero, ndi nyengo zoikika zosekerera; chifukwa chake kondani choonadi ndi mtendere.


Pakuti maso a Ambuye ali pa olungama, ndi makutu ake akumva pembedzo lao; koma nkhope ya Ambuye ili pa ochita zoipa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa