Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 13:5 - Buku Lopatulika

5 Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Mtima wanu usakonde ndalama koma mukhutitsidwe ndi zimene muli nazo, chifukwa Mulungu anati, “Sadzakusiyani, kapena kukutayani konse.”

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 13:5
46 Mawu Ofanana  

Taonani, Ine ndili pamodzi ndi iwe, ndipo ndidzakusunga iwe konse kumene upitako, ndipo ndidzakubwezanso iwe ku dziko lino; chifukwa kuti sindidzakusiya iwe, kufikira kuti nditachita chimene ndanena nawe.


Ndipo iye anati, Ndikupatsa iwe bwanji? Ndipo Yakobo anati, Usandipatse ine kanthu; ukandichitira ine chotero, ine ndidzadyetsanso ndi kusunganso ziweto zako.


ndipo anati kwa iwo, Ndiona ine nkhope ya atate wanu kuti siindionekere ine monga kale; koma Mulungu wa atate wanga anali ndi ine.


Ndipo ndidzakhala pakati pa ana a Israele osawasiya anthu anga a Israele.


Yehova Mulungu wathu akhale nafe monga umo anakhalira nao makolo athu, asatisiye kapena kutitaya;


Ndipo Davide anati kwa Solomoni mwana wake, Limbika, nulimbe mtima, nuchichite; usaopa, kapena kutenga nkhawa; pakuti Yehova Mulungu, ndiye Mulungu wanga, ali nawe; sadzakusowa kapena kukutaya mpaka zitatha ntchito zonse za utumiki wa nyumba ya Yehova.


Pakuti woipa adzitamira chifuniro cha moyo wake, adalitsa wosirira, koma anyoza Yehova.


Lingitsani mtima wanga kumboni zanu, si ku chisiriro ai.


Ndinali mwana ndipo ndakalamba; ndipo sindinapenye wolungama atasiyidwa, kapena mbumba zake zilinkupempha chakudya.


Pakuti Yehova akonda chiweruzo, ndipo sataya okondedwa ake. Asungika kosatha, koma adzadula mbumba za oipa.


Ndipo Mose anavomera kukhala naye munthuyo; ndipo anampatsa Mose mwana wake wamkazi Zipora.


Usasirire nyumba yake ya mnzako, usasirire mkazi wake wa mnzako, kapena wantchito wake wa mwamuna, kapena wantchito wake wamkazi, kapena ng'ombe yake, kapena bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mnzako.


Usadzitopetse kuti ulemere; leka nzeru yakoyako.


usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.


Wosauka ndi wosowa afuna madzi, ndipo palibe, ndi lilime lao lilephera, chifukwa cha ludzu; Ine Yehova ndidzawayankha, Ine Mulungu wa Israele sindidzawasiya.


Ndipo ndidzayendetsa akhungu m'khwalala, limene iwo salidziwa, m'njira zimene iwo sazidziwa ndidzawatsogolera; ndidzawalitsa mdima m'tsogolo mwao, ndi kulungamitsa malo okhota. Zinthu izi Ine ndidzachita, ndipo sindidzawasiya.


Pakuti kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu onse akhala akusirira; ndiponso kuyambira mneneri kufikira wansembe onse achita monyenga.


Ndipo akudzera monga amadzera anthu, nakhala pansi pamaso pako ngati anthu anga, namva mau ako, koma osawachita; pakuti pakamwa pao anena mwachikondi, koma mtima wao utsata phindu lao.


Musadzikundikire nokha chuma padziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri ziononga; ndi pamene mbala ziboola ndi kuba:


Chifukwa chake ndinena kwa inu, Musadere nkhawa moyo wanu, chimene mudzadya ndi chimene mudzamwa; kapena thupi lanu, chimene mudzavala. Kodi moyo suli woposa chakudya, ndi thupi loposa chovala?


Chifukwa chake musadere nkhawa za mawa; pakuti mawa adzadzidera nkhawa iwo okha. Zikwanire tsiku zovuta zake.


zakuba, zakupha, zachigololo, masiriro, zoipa, chinyengo, chinyanso, diso loipa, mwano, kudzikuza, kupusa:


Ndipo asilikali omwe anamfunsa iye, nati, Nanga ife tizichita chiyani? Ndipo iye anati kwa iwo, Musaopse, musanamize munthu aliyense; khalani okhuta ndi kulipira kwanu.


Ndipo zija zinagwa kumingazi, ndiwo amene adamva, ndipo m'kupita kwao atsamwitsidwa ndi nkhawa, ndi chuma, ndi zokondweretsa za moyo, ndipo sakhwimitsa zipatso zamphumphu.


anadzala ndi zosalungama zonse, kuipa, kusirira, dumbo; odzala ndi kaduka, mbanda, ndeu, chinyengo, udani;


koma tsopano ndalembera inu kuti musayanjane naye, ngati wina wotchedwa mbale ali wachigololo, kapena wosirira, kapena wopembedza mafano, kapena wolalatira, kapena woledzera, kapena wolanda, kungakhale kukadya naye wotere, iai.


kapena ambala, kapena osirira, kapena oledzera, kapena olalatira, kapena olanda, sadzalowa Ufumu wa Mulungu.


olondoleka, koma osatayika; ogwetsedwa, koma osaonongeka;


Koma dama ndi chidetso chonse, kapena chisiriro, zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima;


Pakuti ichi muchidziwe kuti wadama yense, kapena wachidetso, kapena wosirira, amene apembedza mafano, alibe cholowa mu ufumu wa Khristu ndi Mulungu.


Khalani amphamvu, limbikani mitima, musamachita mantha, kapena kuopsedwa chifukwa cha iwowa; popeza Yehova Mulungu wanu ndiye amene amuka nanu; Iye sadzakusowani, kapena kukusiyani.


Ndipo Yehova, Iye ndiye amene akutsogolera; Iye adzakhala ndi iwe, Iye sadzakusowa kapena kukusiya; usamachita mantha, usamatenga nkhawa.


popeza Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu wachifundo; sadzakusiyani, kapena kukuonongani, kapena kuiwala chipangano cha makolo anu chimene analumbirira iwo.


Chifukwa chake fetsani ziwalozo zili padziko; dama, chidetso, chifunitso chamanyazi, chilakolako choipa, ndi chisiriro, chimene chili kupembedza mafano;


wosati woledzera, kapena womenyana ndeu; komatu wofatsa, wopanda ndeu, wosakhumba chuma;


Palibe munthu adzatha kuima pamaso pako masiku onse a moyo wako; monga ndinakhala ndi Mose momwemo ndidzakhala ndi iwe; sindidzakusowa, sindidzakusiya.


pamene ndinaona pazofunkha malaya abwino a ku Babiloni, ndi masekeli mazana awiri a siliva, ndi chikute chagolide, kulemera kwake masekeli makumi asanu, ndinazikhumbira ndi kuzitenga; ndipo taonani, ndazibisa m'nthaka pakati pa hema wanga, ndi siliva pansi pakepo.


okhala nao maso odzala ndi chigololo, osakhoza kuleka uchimo, kunyengerera iwo a moyo wosakhazikika; okhala nao mtima wozolowera kusirira; ana a temberero;


Ndipo m'chisiriro adzakuyesani malonda ndi mau onyenga; amene chiweruzo chao sichinachedwe ndi kale lomwe, ndipo chitayiko chao sichiodzera.


Tsoka kwa iwo! Pakuti anayenda m'njira ya Kaini, ndipo anadziononga m'chisokero cha Balamu chifukwa cha kulipira, natayika m'chitsutsano cha Kora.


Ndipo zitakufikirani zizindikiro izi mudzachita monga mudzaona pochita, pakuti Mulungu ali nanu.


Pakuti Yehova sadzasiya anthu ake chifukwa cha dzina lake lalikulu; pakuti kudamkomera Yehova kukuyesani inu anthu a Iye yekha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa