Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 37:34 - Buku Lopatulika

34 Yembekeza Yehova, nusunge njira yake, ndipo Iye adzakukweza kuti ulandire dziko. Pakudulidwa oipa udzapenya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

34 Yembekeza Yehova, nusunge njira yake, ndipo Iye adzakukweza kuti ulandire dziko. Pakudulidwa oipa udzapenya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

34 Khulupirira Chauta, ndipo usunge njira zake. Motero adzakukweza ndipo udzalandira dziko kuti likhale lako. Udzaona anthu oipa akuwonongeka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

34 Khulupirira Yehova, ndipo sunga njira yake; Iye adzakukweza ndipo udzalandira dziko kuti likhale lako; udzaona anthu oyipa akuwonongeka.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 37:34
23 Mawu Ofanana  

Koma wolungama asungitsa njira yake, ndi iye wa manja oyera adzakulabe mumphamvu.


Mtima wake ngwochirikizika, sadzachita mantha, kufikira ataona chofuna iye pa iwo omsautsa.


Anagawagawa, anapatsa aumphawi; chilungamo chake chikhalitsa kosatha; nyanga yake idzakwezeka ndi ulemu.


Moyo wake udzakhala mokoma; ndi mbumba zake zidzalandira dziko lapansi.


Yembekeza Yehova, limbika, ndipo Iye adzalimbitsa mtima wako; inde, yembekeza Yehova.


Khulupirira Yehova, ndipo chita chokoma; khala m'dziko, ndipo tsata choonadi.


Khala chete mwa Yehova, numlindirire Iye; usavutike mtima chifukwa cha iye wolemerera m'njira yake, chifukwa cha munthu wakuchita chiwembu.


Pakuti ochita zoipa adzadulidwa; koma iwo akuyembekeza Yehova, iwowa adzalandira dziko lapansi.


Koma udzapenya ndi maso ako, nudzaona kubwezera chilango oipa.


Wolungama adzaphuka ngati mgwalangwa; adzakula ngati mkungudza wa ku Lebanoni.


Khwalala la oongoka mtima ndilo lakuti asiye zoipa; wosunga njira yake atchinjiriza moyo wake.


Usanene, Ndidzabwezera zoipa; yembekeza Yehova, adzakupulumutsa.


Pochuluka oipa zolakwa zichuluka; koma olungama adzaona kugwa kwao.


Pamene pakufuula iwe akupulumutse amene unawasonkhanitsa; koma mphepo idzawatenga, mpweya udzachotsa onse; koma iye amene andikhulupirira Ine adzakhala ndi dziko, nadzakhala nacho cholowa m'phiri langa lopatulika.


Koma iye wakulimbika chilimbikire kufikira kuchimaliziro, yemweyo adzapulumuka.


Chifukwa munthu aliyense wakudzikuza adzachepetsedwa; ndipo wakudzichepetsa adzakulitsidwa.


Muziyenda m'njira yonse imene Yehova Mulungu wanu anakulamulirani, kuti mukakhale ndi moyo, ndi kuti chikukomereni, ndi kuti masiku anu achuluke m'dziko limene mudzakhala nalo lanulanu.


kuti mayesedwe a chikhulupiriro chanu, ndiwo a mtengo wake woposa wa golide amene angotayika, ngakhale ayesedwa ndi moto, akapezedwe ochitira chiyamiko ndi ulemerero ndi ulemu pa vumbulutso la Yesu Khristu;


Potero dzichepetseni pansi padzanja la mphamvu la Mulungu, kuti panthawi yake akakukwezeni;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa