Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 106:3 - Buku Lopatulika

3 Odala iwo amene asunga chiweruzo, iye amene achita chilungamo nthawi zonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Odala iwo amene asunga chiweruzo, iye amene achita chilungamo nthawi zonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Ngodala anthu otsata malamulo a Chauta, anthu ochita zolungama nthaŵi zonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Odala ndi amene amasunga chilungamo, amene amachita zolungama nthawi zonse.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 106:3
29 Mawu Ofanana  

Ndinalumbira, ndipo ndinatsimikiza mtima, kuti ndidzasamalira maweruzo anu olungama.


Ndinalingitsa mtima wanga uchite malemba anu, kosatha, kufikira chimaliziro.


Mtima wanga wasweka ndi kukhumba maweruzo anu nyengo zonse.


Potero ndidzasamalira malamulo anu chisamalire kunthawi za nthawi.


Iye wakuyendayo mokwanira, nachita chilungamo, nanena zoonadi mumtima mwake.


Musakumbukire zolakwa za ubwana wanga kapena zopikisana nanu. Mundikumbukire monga mwa chifundo chanu, chifukwa cha ubwino wanu, Yehova.


Inu mukomana ndi iye amene akondwerera, nachita chilungamo, iwo amene akumbukira Inu m'njira zanu; taonani Inu munakwiya, ndipo ife tinachimwa; takhala momwemo nthawi yambiri, kodi tidzapulumutsidwa?


Pakuti aliyense achita chifuniro cha Mulungu, yemweyo ndiye mbale wanga, ndi mlongo, ndi amai.


Koma Iye anati, Inde, koma odala iwo akumva mau a Mulungu, nawasunga.


Koma tsoka inu, Afarisi! Chifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbeu tonunkhira, ndi timbeu tokometsa chakudya ndi ndiwo zonse, ndipo mumaleka chiweruzo ndi chikondi cha Mulungu; mwenzi mutachita izi, ndi kusasiya zinazo.


Ngati mudziwa izi, odala inu ngati muzichita.


Muli abwenzi anga inu, ngati muzichita zimene ndikulamulani inu.


M'menemonso ndidziyesera ndekha ndikhale nacho nthawi zonse chikumbumtima chosanditsutsa cha kwa Mulungu ndi kwa anthu.


kwa iwo amene afunafuna ulemerero ndi ulemu ndi chisaonongeko, mwa kupirira pa ntchito zabwino, adzabwezera moyo wosatha;


Koma tisaleme pakuchita zabwino; pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka.


Chifukwa chake muzikonda Yehova Mulungu wanu, ndi kusunga chilangizo chake, ndi malemba ake, ndi maweruzo ake, ndi malamulo ake, masiku onse.


Koma iye wakupenyerera m'lamulo langwiro, ndilo laufulu, natero chipenyerere, ameneyo, posakhala wakumva wakuiwala, komatu wakuchita ntchito, adzakhala wodala m'kuchita kwake.


Odala iwo amene atsuka miinjiro yao, kuti akakhale nao ulamuliro pa mtengo wa moyo, ndi kuti akalowe m'mzinda pazipata.


Chifukwa chake ali kumpando wachifumu wa Mulungu; ndipo amtumikira Iye usana ndi usiku mu Kachisi mwake; ndipo Iye wakukhala pa mpando wachifumu adzawachitira mthunzi,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa