Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Akorinto 5:21 - Buku Lopatulika

21 Ameneyo sanadziwe uchimo anamyesera uchimo m'malo mwathu; kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa Iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Ameneyo sanadziwa uchimo anamyesera uchimo m'malo mwathu; kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa Iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Khristu sadachimwe konse, koma Mulungu adamsandutsa uchimo chifukwa cha ife, kuti mwa Iyeyo ife tisanduke olungama pamaso pa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Chifukwa cha ife, Mulungu anasandutsa wopanda tchimoyo kukhala tchimo, kuti mwa Iye ife tikakhale chilungamo cha Mulungu.

Onani mutuwo Koperani




2 Akorinto 5:21
30 Mawu Ofanana  

Ichi chidzakhala masiku angati m'mtima mwa aneneri amene anenera zonama; ndiwo aneneri a chinyengo cha mtima wao?


Masiku omwewo Yuda adzapulumutsidwa, ndi Yerusalemu adzakhala mokhulupirika; ili ndi dzina adzatchedwa nalo, Yehova ndiye chilungamo chathu.


Masabata makumi asanu ndi awiri alamulidwira anthu a mtundu wako ndi mzinda wako wopatulika, kumaliza cholakwacho, ndi kutsiriza machimo, ndi kutetezera mphulupulu, ndi kufikitsa chilungamo chosalekeza, ndi kukhomera chizindikiro masomphenya ndi zonenera, ndi kudzoza malo opatulika kwambiri.


Ndipo atapita masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri wodzozedwayo adzalikhidwa, nadzakhala wopanda kanthu; ndi anthu a kalonga wakudzayo adzaononga mzinda ndi malo opatulika; ndi kutsiriza kwake kudzakhala kwa chigumula, ndi kufikira chimaliziro kudzakhala nkhondo; chipasuko chalembedweratu.


Galamuka, lupanga, pa mbusa wanga, ndi pa munthu mnzanga wa pamtima, ati Yehova wa makamu; kantha mbusa, ndi nkhosa zidzabalalika; koma ndidzabwezera dzanja langa pa zazing'onozo.


Ndipo Mose anapanga njoka yamkuwa, naiika pamtengo; ndipo kunali, njoka itamluma munthu aliyense, nakapenyetsetsa iye pa njoka yamkuwa, nakhala ndi moyo.


ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza;


tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo;


Ndipo mngelo anayankha, nati kwa iye, Mzimu Woyera adzafika pa iwe, ndi mphamvu ya Wamkulukulu idzakuphimba iwe: chifukwa chakenso Choyeracho chikadzabadwa, chidzatchedwa Mwana wa Mulungu.


Koma inu munakaniza Woyera ndi Wolungamayo, ndipo munapempha kuti munthu wambanda apatsidwe kwa inu,


Pakuti m'menemo chaonetsedwa chilungamo cha Mulungu chakuchokera kuchikhulupiriro kuloza kuchikhulupiriro: monga kwalembedwa, Koma munthu wolungama adzakhala ndi moyo ndi chikhulupiriro.


amene anaperekedwa chifukwa cha zolakwa zathu, naukitsidwa chifukwa cha kutiyesa ife olungama.


Pakuti monga ndi kusamvera kwa munthu mmodzi ambiri anayesedwa ochimwa, chomwecho ndi kumvera kwa mmodzi ambiri adzayesedwa olungama.


Koma kwa Iye muli inu mwa Khristu Yesu, amene anayesedwa kwa ife nzeru ya kwa Mulungu, ndi chilungamo ndi chiyeretso ndi chiombolo;


Chifukwa chake ngati munthu aliyense ali mwa Khristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano.


Khristu anatiombola ku temberero la chilamulo, atakhala temberero m'malo mwathu; pakuti kwalembedwa, Wotembereredwa aliyense wopachikidwa pamtengo.


ndipo yendani m'chikondi monganso Khristu anakukondani inu, nadzipereka yekha m'malo mwathu, chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale fungo lonunkhira bwino.


ndi kupezedwa mwa Iye, wosati wakukhala nacho chilungamo changa cha m'lamulo, koma chimene cha mwa chikhulupiriro cha Khristu, chilungamocho chochokera mwa Mulungu ndi chikhulupiriro;


Pakuti sitili naye mkulu wa ansembe wosatha kumva chifundo ndi zofooka zathu; koma wayesedwa m'zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo.


Pakuti mkulu wa ansembe wotere anatiyenera ife, woyera mtima, wopanda choipa, wosadetsedwa, wosiyana ndi ochimwa, wakukhala wopitirira miyamba;


Pakuti Khristunso adamva zowawa kamodzi, chifukwa cha machimo, wolungama m'malo mwa osalungama, kuti akatifikitse kwa Mulungu; wophedwatu m'thupi, koma wopatsidwa moyo mumzimu;


Ndipo mudziwa kuti Iyeyu anaonekera kudzachotsa machimo; ndipo mwa Iye mulibe tchimo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa