20 Chifukwa chake tili atumiki m'malo mwa Khristu, monga ngati Mulungu alikudandaulira mwa ife; tiumiriza inu m'malo mwa Khristu, yanjanitsidwani ndi Mulungu.
20 Chifukwa chake tili atumiki m'malo mwa Khristu, monga ngati Mulungu alikudandaulira mwa ife; tiumiriza inu m'malo mwa Khristu, yanjanitsidwani ndi Mulungu.
20 Choncho ife ndi akazembe a Khristu, monga ngati Mulungu akudandaulira anthu kudzera mwa ife. Ife tikukupemphani inu mʼmalo mwa Khristu kuti, yanjanitsidwani ndi Mulungu.
Ndipo Yehova anachitira umboni Israele ndi Yuda mwa dzanja la mneneri aliyense, ndi mlauli aliyense, ndi kuti, Bwererani kuleka ntchito zanu zoipa, nimusunge malamulo anga ndi malemba anga, monga mwa chilamulo chonse ndinachilamulira makolo anu, ndi kuchitumizira inu mwa dzanja la atumiki anga aneneri.
Ndipo Yehova Mulungu wa makolo ao anatumiza kwa iwo ndi dzanja la mithenga yake, nalawirira mamawa kuituma, chifukwa anamvera chifundo anthu ake, ndi pokhala pake;
Pakuti milomo ya wansembe iyenera kusunga chidziwitso, ndi anthu ayenera kufunafuna chilamulo pakamwa pake; pakuti iye ndiye mthenga wa Yehova wa makamu.
Pakuti ngati, pokhala ife adani ake, tinayanjanitsidwa ndi Mulungu mwa imfa ya Mwana wake, makamaka ndithu, popeza ife tayanjanitsidwa, tidzapulumuka ndi moyo wake.