Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 18:20 - Buku Lopatulika

20 Yehova anandibwezera monga mwa chilungamo changa; anandisudzula monga mwa kusisira kwa manja anga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Yehova anandibwezera monga mwa chilungamo changa; anandisudzula monga mwa kusisira kwa manja anga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Chauta adandipatsa mphotho molingana ndi ntchito zanga zabwino, adandifupa molingana ndi ungwiro wanga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Yehova wandithandiza molingana ndi chilungamo changa; molingana ndi makhalidwe anga abwino, Iye wandipulumutsa.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 18:20
19 Mawu Ofanana  

Adzamasula ngakhale wopalamula, inde adzamasuka mwa kuyera kwa manja ako.


Inde akadakukopani muchoke posaukira, mulowe kuchitando kopanda chopsinja; ndipo zoikidwa pagome panu zikadakhala zonona ndithu.


M'mene ndinasautsika ndinaitanira pa Yehova; anandiyankha nandiika motakasuka Yehova.


Ndimo anandisudzulira Yehova monga mwa chilungamo changa, monga mwa kusisira kwa manja anga pamaso pake.


Woyera m'manja, ndi woona m'mtima, ndiye; iye amene sanakweze moyo wake kutsata zachabe, ndipo salumbira monyenga.


Ndidzasamba manja anga mosalakwa; kuti ndizungulire guwa la nsembe lanu, Yehova;


Mundichitire chifundo, Yehova, pakuti ndasautsika ine. Diso langa, mzimu wanga, ndi mimba yanga, zapuwala ndi mavuto.


Ndipo anthu adzati, Indedi, pali mphotho kwa wolungama. Indedi, pali Mulungu wakuweruza padziko lapansi.


Yehova Mulungu wanga, ngati ndachita ichi; ngati m'manja anga muli chosalungama;


Yehova aweruza anthu mlandu; mundiweruze, Yehova, monga mwa chilungamo changa, ndi ungwiro wanga uli mwa ine.


Woipa alandira malipiro onyenga; koma wofesa chilungamo aonadi mphotho.


Koma ndinati, Ndagwira ntchito mwachabe, ndatha mphamvu zanga pachabe, ndi mopanda pake; koma ndithu chiweruziro changa chili ndi Yehova, ndi kubwezera kwanga kuli ndi Mulungu wanga.


Taonani, Yehova walalikira kufikira malekezero a dziko lapansi. Nenani kwa mwana wamkazi wa Ziyoni, Taona chipulumutso chako chifika; taona mphotho yake ali nayo, ndi ntchito yake ili pamaso pake.


kotero kuti mphatso zako zachifundo zikhale zam'tseri; ndipo Atate wako wakuona m'tseri adzakubwezera iwe.


Koma wookayo ndi wothirirayo ali amodzi; koma yense adzalandira mphotho yake ya iye yekha, monga mwa kuchititsa kwake kwa iye yekha.


Pakuti mkulu wa ansembe wotere anatiyenera ife, woyera mtima, wopanda choipa, wosadetsedwa, wosiyana ndi ochimwa, wakukhala wopitirira miyamba;


Nati kwa Davide, Iwe ndiwe wolungama woposa ine; popeza unandibwezera zabwino, koma ine ndinakubwezera zoipa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa