Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 18:21 - Buku Lopatulika

21 Pakuti ndasunga njira za Yehova, ndipo sindinachitire choipa kusiyana ndi Mulungu wanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Pakuti ndasunga njira za Yehova, ndipo sindinachitira choipa kusiyana ndi Mulungu wanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Ine ndidatsata njira za Chauta, sindidachite zoipa ndi kumsiya Mulungu wanga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Pakuti ine ndinatsata njira za Yehova; ndilibe mlandu wochoka pamaso Mulungu wanga.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 18:21
13 Mawu Ofanana  

Ndipo anayenda m'njira ya Asa atate wake osapatukamo, nachita zoongoka pamaso pa Yehova.


Yosiya nachotsa zonyansa zonse m'maiko onse okhala a ana a Israele, natumikiritsa onse opezeka mu Israele, inde kutumikira Yehova Mulungu wao. Masiku ake onse iwo sanapatuke kusamtsata Yehova Mulungu wa makolo ao.


Sindinapatukane nao maweruzo anu; pakuti Inu munandiphunzitsa.


Za machitidwe a anthu, ndachenjera ndi mau a milomo yanu ndingalowe njira za woononga.


Mundiweruze, Yehova, pakuti ndayenda mu ungwiro wanga, ndipo ndakhulupirira Yehova, sindadzaterereka.


Ithe mphulupulu ya anthu oipa, ndikupemphani, koma wolungamayo mumkhazikitse. Pakuti woyesa mitima ndi impso ndiye Mulungu wolungama.


Ndipo tsopano, ananga, mundimvere ine, ngodala akusunga njira zanga.


Pamenepo mfumu inakondwera kwambiri, niwauza atulutse Daniele m'dzenje. Momwemo anamtulutsa Daniele m'dzenje, ndi pathupi pake sipadaoneke bala, popeza anakhulupirira Mulungu wake.


M'menemonso ndidziyesera ndekha ndikhale nacho nthawi zonse chikumbumtima chosanditsutsa cha kwa Mulungu ndi kwa anthu.


Inu ndinu mboni, Mulungunso, kuti tinakhala oyera mtima ndi olungama ndi osalakwa kwa inu akukhulupirira;


Anatuluka mwa ife, komatu sanali a ife; pakuti akadakhala a ife akadakhalabe ndi ife, koma kudatero kuti aonekere kuti sali onse a ife.


Kundichititsa chisoni kuti ndinaika Saulo akhale mfumu; pakuti wabwerera wosanditsata Ine, ndipo sanachite malamulo anga. Ndipo Samuele anakwiya; nalira kwa Yehova usiku wonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa