Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 119:11 - Buku Lopatulika

11 Ndinawabisa mau anu mumtima mwanga, kuti ndisalakwire Inu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndinawabisa mau anu mumtima mwanga, kuti ndisalakwire Inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Ndasunga mau anu mumtima mwanga, kuti ndisakuchimwireni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Ndasunga mawu anu mu mtima mwanga kuti ndisakuchimwireni.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 119:11
13 Mawu Ofanana  

Landira tsono chilamulo pakamwa pake, nuwasunge maneno ake mumtima mwako.


Komatu m'chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake; ndipo m'chilamulo chake amalingirira usana ndi usiku.


Ha! Ndikondadi chilamulo chanu; ndilingiriramo ine tsiku lonse.


Ndiponso muletse kapolo wanu pa zodzitama; zisachite ufumu pa ine. Pamenepo ndidzakhala wangwiro, ndi wosachimwa cholakwa chachikulu.


Malamulo a Mulungu wake ali mumtima mwake; pakuyenda pake sadzaterereka.


kuchita chikondwero chanu kundikonda, Mulungu wanga; ndipo malamulo anu ali m'kati mwamtima mwanga.


Mwananga, ukalandira mau anga, ndi kusunga malamulo anga;


Mverani Ine, inu amene mudziwa chilungamo, anthu amene mumtima mwao muli lamulo langa; musaope chitonzo cha anthu, ngakhale kuopsedwa ndi kutukwana kwao.


Mau anu anapezeka, ndipo ndinawadya; mau anu anakhala kwa ine chikondwero ndi chisangalalo cha mtima wanga; pakuti ndatchedwa dzina lanu, Yehova Mulungu wa makamu.


Koma Maria anasunga mau awa onse, nawalingalira mumtima mwake.


Ndipo anatsika nao pamodzi nadza ku Nazarete; nawamvera iwo: ndipo amake anasunga zinthu izi zonse mumtima mwake.


Mau a Khristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalimo, ndi mayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuimbira Mulungu ndi chisomo mumtima mwanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa