Yeremiya 14:10 - Buku Lopatulika10 Atero Yehova kwa anthu awa, Chomwecho akonda kusocherera; sanakanize mapazi ao; chifukwa chake Yehova sawalandira; tsopano adzakumbukira choipa chao, nadzalanga zochimwa zao. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 Atero Yehova kwa anthu awa, Chomwecho akonda kusocherera; sanakanize mapazi ao; chifukwa chake Yehova sawalandira; tsopano adzakumbukira choipa chao, nadzalanga zochimwa zao. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 Chauta akunena za anthu ameneŵa kuti, “Amakonda kuyendayenda kumene afuna, ndipo sangathe kudziletsa. Nchifukwa chake Ine Chauta sindingakondwere nawo, ndipo tsopano ndidzakumbukira kuipa kwao, ndidzaŵalanga chifukwa cha machimo ao.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 Zimene Yehova akunena za anthuwa ndi izi: “Iwo amakonda kuyendayenda kwambiri; samatha kudziretsa. Nʼchifukwa chake Ine Yehova sindingawalandire, ndipo tsopano ndidzakumbukira zoyipa zawo ndi kuwalanga chifukwa cha machimo awo.” Onani mutuwo |