Mtima wanga ukudzaza ndi mtendere wosatheka, mtendere umene ukubweretsa bata ndi mpumulo m'moyo wanga. Ndikudziwa kuti ndadalitsidwa ndi Mulungu, ndipo zimenezi zimandipatsa chimwemwe chachikulu moti ndimangofuna kuyamika. Mtima wanga umakhudzidwa kwambiri ndikamaona zodabwitsa za Mulungu, ndipo ndimazindikira kukoma mtima kwake pa ine.
Chifukwa cha zimenezi, kutumikira Mulungu ndi njira yochepa yothokozera zonse zimene wandichitira. Kale ndinali mu mdima, ndinali pansi pa temberero la uchimo, koma nditalandira Yesu ngati Mpulumutsi wanga, ndinaomboledwa ku tembererolo. Magazi a Yesu amasandutsa chitemberero kukhala dalitso.
Monga momwe lemba la Aefeso 2:5 limanenera, "Tinali akufa m'machimo athu, koma Mulungu anatipatsa moyo pamodzi ndi Khristu. Mwa chisomo chake mudapulumutsidwa." Ndiyenera kukumbukira kuti ndinabadwira kukhala dalitso mulimonse mmene zinthu zilili. Ndinedi munthu wodzipereka kwa Mulungu, wodzazidwa ndi chisomo chake ndi chiyanjo chake.
Sindiyenera kulola mawu ena aliwonse otsutsana ndi Mzimu Woyera wa Mulungu. Sindine cholakwika kapena ngozi; ndili m'dziko lino kudalitsa miyoyo ya anthu m'dzina la Yesu.
Luka 6:27-28 amati, "Koma kwa inu akumva, ndikukuuzani, kondani adani anu, chitani zabwino kwa iwo amene amakudani, dalitsani iwo amene amakutukwanani, pemphererani iwo amene amakupwetekani." Dziko lino silikufuna matemberero; monga mwana wa Mulungu, ndiyenera kuyimirira ndi kutsegula pakamwa panga kudalitsa, kulengeza machiritso pakati pa matenda, kulankhula za moyo m'malo mwa imfa, ndi kulengeza chipulumutso pamene ambiri alengeza chiwonongeko.
Mulungu akufuna kuti ndikhale chitsime cha madalitso kwa ambiri.
Yehova akudalitse iwe, nakusunge;
Yehova awalitse nkhope yake pa iwe, nakuchitire chisomo;
Yehova akweze nkhope yake pa iwe, nakupatse mtendere.
Atichitire chifundo Mulungu, ndi kutidalitsa, atiwalitsire nkhope yake;
kuti njira yanu idziwike padziko lapansi, chipulumutso chanu mwa amitundu onse.
Ndipo kudzali, mukadzamvera mau a Yehova Mulungu wanu mwachangu, ndi kusamalira kuchita malamulo ake onse amene ndikuuzani lero, kuti Yehova Mulungu wanu adzakukulitsani koposa amitundu onse a padziko lapansi;
Ndipo anthu onse a padziko lapansi adzaona kuti akutchulani dzina la Yehova; nadzakuopani.
Ndipo Yehova adzakuchulukitsirani zokoma, m'zipatso za thupi lanu, ndi m'zipatso za zoweta zanu, ndi m'zipatso za nthaka yanu, m'dziko limene Yehova analumbirira makolo anu kuti adzakupatsani ilo.
Yehova adzakutsegulirani chuma chake chokoma, ndicho thambo la kumwamba, kupatsa dziko lanu mvula m'nyengo yake, ndi kudalitsa ntchito zonse za dzanja lanu; ndipo mudzakongoletsa amitundu ambiri, osakongola nokha.
Ndipo Yehova adzakuyesani mutu, si mchira ai; ndipo mudzakhala wa pamwamba pokha, si wapansi ai; ngati mudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu, amene ndikuuzani lero, kuwasunga ndi kuwachita;
osapatukira mau ali onse ndikuuzani lero, kulamanja, kapena kulamanzere, kutsata milungu ina kuitumikira.
Koma kudzali, mukapanda kumvera mau a Yehova Mulungu wanu, kusamalira kuchita malamulo ake onse ndi malemba ake amene ndikuuzani lero, kuti matemberero awa onse adzakugwerani ndi kukupezani.
Mudzakhala otembereredwa m'mzinda, ndi otembereredwa pabwalo.
Lidzakhala lotembereredwa dengu lanu ndi choumbiramo mkate wanu.
Zidzakhala zotembereredwa zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, zoswana za ng'ombe zanu, ndi zoswana za nkhosa zanu.
Mudzakhala otembereredwa polowa inu, ndi otembereredwa potuluka inu.
ndipo madalitso awa onse adzakugwerani, ndi kukupezani, mukadzamvera mau a Yehova Mulungu wanu.
Wodala yense wakuopa Yehova, wakuyenda m'njira zake.
Pakuti udzadya za ntchito ya manja ako; wodala iwe, ndipo kudzakukomera.
ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kubukitsa dzina lako; nukhale iwe mdalitso;
Ndipo Farao analamulira anthu ake za iye; ndipo anamperekeza iye m'njira ndi mkazi wake ndi zonse anali nazo.
ndipo ndidzadalitsa amene akudalitsa iwe; ndi kutemberera iye amene akutemberera iwe; ndipo mwa iwe adzadalitsidwa mabanja onse a dziko lapansi.
Pakuti ndidziwa malingiriro amene ndilingiririra inu, ati Yehova, malingiriro a mtendere, si a choipa, akukupatsani inu adzukulu ndi chiyembekezero.
Ndipo muzitumikira Yehova Mulungu wanu, potero adzadalitsa chakudya chako, ndi madzi ako; ndipo ndidzachotsa nthenda pakati pa iwe.
Ndipo ndidziwa kuti pamene ndikadza kwanu, ndidzafika m'kudzaza kwake kwa chidalitso cha Khristu.
Aleluya. Wodala munthu wakuopa Yehova, wakukondwera kwambiri ndi malamulo ake.
Woipa adzaziona, nadzapsa mtima; adzakukuta mano, nadzasungunuka; chokhumba oipa chidzatayika.
Mbeu yake idzakhala yamphamvu padziko lapansi; mbadwo wa oongoka mtima udzadalitsidwa.
M'nyumba mwake mudzakhala akatundu ndi chuma: Ndi chilungamo chake chikhala chikhalire.
popeza ndikuuzani lero kukonda Yehova Mulungu wanu, kuyenda m'njira zake, ndi kusunga malamulo ake ndi malemba ake ndi maweruzo ake, kuti mukakhale ndi moyo ndi kuchuluka, ndi kuti Yehova Mulungu wanu akakudalitseni m'dziko limene mulowako kulilandira.
Odala ali oyera mtima; chifukwa adzaona Mulungu.
Odala ali akuchita mtendere; chifukwa adzatchedwa ana a Mulungu.
Koma ndinena kwa inu akumva, Kondanani nao adani anu; chitirani zabwino iwo akuda inu,
dalitsani iwo akutemberera inu, pemphererani iwo akuchitira inu chipongwe.
usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.
Ndipo Mulungu akhoza kuchulukitsira chisomo chonse kwa inu; kuti inu, pokhala nacho chikwaniro chonse m'zinthu zonse, nthawi zonse, mukachulukire kuntchito yonse yabwino;
osabwezera choipa ndi choipa, kapena chipongwe ndi chipongwe, koma penatu madalitso; pakuti kudzatsata ichi mwaitanidwa, kuti mukalandire dalitso.
Mudzandidziwitsa njira ya moyo, pankhope panu pali chimwemwe chokwanira; m'dzanja lanu lamanja muli zokondweretsa zomka muyaya.
Ndipo kudzali, mukadzamvera mau a Yehova Mulungu wanu mwachangu, ndi kusamalira kuchita malamulo ake onse amene ndikuuzani lero, kuti Yehova Mulungu wanu adzakukulitsani koposa amitundu onse a padziko lapansi;
Kuti dalitso la Abrahamu mwa Khristu Yesu, lichitike kwa amitundu; kuti tikalandire lonjezano la Mzimuyo, mwa chikhulupiriro.
Popeza Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani, monga ananena nanu; ndipo mudzakongoletsa amitundu ambiri, osakongola nokha; nimudzachita ufumu pa amitundu ambiri, koma iwo sadzachita ufumu pa inu.
polemeretsedwa inu m'zonse kukuolowa manja konse, kumene kuchita mwa ife chiyamiko cha kwa Mulungu.
Pakuti ndidzaika izi ndi midzi yozungulira chitunda changa, zikhale mdalitso; ndipo ndidzavumbitsa mivumbi m'nyengo yake, padzakhala mivumbi ya madalitso.
Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa chosowa chanu chilichonse monga mwa chuma chake mu ulemerero mwa Khristu Yesu.
Mundiyalikira gome pamaso panga m'kuona kwa adani anga; mwandidzoza mutu wanga mafuta; chikho changa chisefuka.
Ndidzalemekeza Yehova nyengo zonse; kumlemekeza kwake kudzakhala m'kamwa mwanga kosalekeza.
Pakuti Yehova Mulungu ndiye dzuwa ndi chikopa; Yehova adzapatsa chifundo ndi ulemerero; sadzakaniza chokoma iwo akuyenda angwiro.
Koma muyambe mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.
Iye amene akhala pansi m'ngaka yake ya Wam'mwambamwamba adzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse.
palibe choipa chidzakugwera, ndipo cholanga sichidzayandikiza hema wako.
Pakuti adzalamulira angelo ake za iwe, akusunge m'njira zako zonse.
Adzakunyamula pa manja ao, ungagunde phazi lako pamwala.
Udzaponda mkango ndi mphiri; udzapondereza msona wa mkango ndi chinjoka.
Popeza andikondadi ndidzampulumutsa; ndidzamkweza m'mwamba, popeza adziwa dzina langa.
Adzandifuulira Ine ndipo ndidzamyankha; kunsautso ndidzakhala naye pamodzi; ndidzamlanditsa, ndi kumchitira ulemu.
Ndidzamkhutitsa ndi masiku ambiri, ndi kumuonetsera chipulumutso changa.
Ndidzati kwa Yehova, Pothawirapo panga ndi linga langa; Mulungu wanga, amene ndimkhulupirira.
Mochokera m'kamwa momwemo mutuluka chiyamiko ndi temberero. Abale anga, izi siziyenera kutero.
Maso a onse ayembekeza Inu; ndipo muwapatsa chakudya chao m'nyengo zao.
Muolowetsa dzanja lanu, nimukwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chao.
Pakuti Inu, Yehova, mudzadalitsa wolungamayo; mudzamtchinjiriza nacho chivomerezo ngati chikopa.
chilichonse mukachichita, gwirani ntchito mochokera mumtima, monga kwa Ambuye, osati kwa anthu ai;
podziwa kuti mudzalandira kwa Ambuye mphotho ya cholowa; mutumikira Ambuye Khristu mwaukapolo.
Pakuti mkwiyo wake ukhala kanthawi kokha; koma kuyanja kwake moyo wonse. Kulira kuchezera, koma mamawa kuli kufuula kokondwera.
Munthu wokhulupirika ali ndi madalitso ambiri; koma wokangaza kulemera sadzapulumuka chilango.
Munthuyo wakuopa Yehova ndani? Adzamlangiza iye njira adzasankheyo.
Moyo wake udzakhala mokoma; ndi mbumba zake zidzalandira dziko lapansi.
Ndipo padzakhala kuti iwo asanaitane Ine, ndidzayankha; ndipo ali chilankhulire, Ine ndidzamva.
Inu, Yehova, Mulungu wanga, zodabwitsa zanu mudazichita nzambiri, ndipo zolingirira zanu za pa ife; palibe wina wozifotokozera Inu; ndikazisimba ndi kuzitchula, zindichulukira kuziwerenga.
Iye amene sanatimane Mwana wake wa Iye yekha, koma anampereka chifukwa cha ife tonse, adzalekeranji kutipatsanso ife zinthu zonse kwaulere pamodzi ndi Iye?
Akubzala ndi misozi adzatuta ndi kufuula mokondwera.
Iye amene ayendayenda nalira, ponyamula mbeu yakufesa; adzabweranso ndithu ndi kufuula mokondwera, alikunyamula mitolo yake.
Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu;
pakuti yense wakupempha alandira; ndi wakufunayo apeza; ndi kwa wogogodayo chitsegulidwa.
Lodala dzina la Yehova Kuyambira tsopano kufikira kosatha.
Chitulukire dzuwa kufikira kulowa kwake lilemekezedwe dzina la Yehova.
Pakuti Mulungu sanatipatse mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi chikondi ndi chidziletso.
Ndi Mulungu wa atate wako amene adzakuthangata iwe, ndi Wamphamvuyonse, amene adzakudalitsa iwe. Ndi madalitso a Kumwamba, madalitso a madzi akuya akukhala pansi, madalitso a mawere, ndi a mimba.
Wodala munthu amene akhala naye Mulungu wa Yakobo kuti amthandize, chiyembekezo chake chili pa Yehova, Mulungu wake.
Wodala munthuyo mumsankha, ndi kumyandikizitsa, akhale m'mabwalo anu. Tidzakhuta nazo zokoma za m'nyumba yanu, za m'malo oyera a Kachisi wanu.
koma wopanda chikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna Iye.
Mau a m'kamwa mwanga ndi maganizo a m'mtima wanga avomerezeke pamaso panu, Yehova, thanthwe langa, ndi Mombolo wanga.
Yehova adzakudalitsa ali mu Ziyoni; ndipo udzaona zokoma za Yerusalemu masiku onse a moyo wako.
Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula; ndipo lilime lonse limene lidzakangana nawe m'chiweruzo udzalitsutsa. Ichi ndi cholowa cha atumiki a Yehova, ndi chilungamo chao chimene chifuma kwa Ine, ati Yehova.
Yehova ndiye gawo la cholowa changa ndi chikho changa, ndinu wondigwirira cholandira changa.
Zingwe zandigwera mondikondweretsa; inde cholowa chokoma ndili nacho.
Wolemekeza Ambuye, tsiku ndi tsiku atisenzera katundu, ndiye Mulungu wa chipulumutso chathu.
Ukulu, ndi mphamvu, ndi ulemerero, ndi chipambano, ndi chifumu ndi zanu, Yehova; pakuti zonse zam'mwamba ndi padziko lapansi ndi zanu; ufumu ndi wanu, Yehova; ndipo mwakwezeka mutu wa pa zonse.
Zolemera ndi ulemu zifuma kwanu, ndipo muchita ufumu pa zonse, ndi m'dzanja mwanu muli mphamvu yaikulu; kukuza ndi kupatsa onse mphamvu kuli m'dzanja lanu.
Amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zili m'mwemo. Ndiye wakusunga choonadi kosatha,
ndikakonzere iwo amene alira maliro mu Ziyoni, ndi kuwapatsa chovala kokometsa m'malo mwa phulusa, mafuta akukondwa m'malo mwa maliro, chovala cha matamando m'malo mwa mzimu wopsinjika; kuti iwo atchedwe mitengo ya chilungamo yakuioka Yehova, kuti Iye alemekezedwe.
Pomwepo Mfumuyo idzanena kwa iwo a kudzanja lake lamanja, Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, lowani mu Ufumu wokonzedwera kwa inu pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi:
Mundigwirizize ndipo ndidzapulumutsidwa, ndipo ndidzasamalira malemba anu chisamalire.
Lamulira iwo achuma m'nthawi ino ya pansi pano, kuti asadzikuze, kapena asayembekezere chuma chosadziwika kukhala kwake, koma Mulungu, amene atipatsa ife zonse kochulukira, kuti tikondwere nazo;
M'nyumba mwake mudzakhala akatundu ndi chuma: Ndi chilungamo chake chikhala chikhalire.
ndipo abwere Mlevi, popeza alibe gawo kapena cholowa pamodzi ndi inu, ndi mlendo, ndi ana amasiye, ndi mkazi wamasiye, okhala m'mudzi mwanu, nadye nakhute; kuti Yehova Mulungu wanu akakudalitseni mu ntchito zonse za dzanja lanu muzichitazi.
koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.
Wodalitsika Yehova, Pakuti adamva mau a kupemba kwanga.
Yehova ndiye mphamvu yanga, ndi chikopa changa; mtima wanga wakhulupirira Iye, ndipo anandithandiza, chifukwa chake mtima wanga ukondwera kwakukulu; ndipo ndidzamyamika nayo nyimbo yanga.
Ndipo anadalitsa iwo tsiku lomwelo, nati, Mwa iwe Israele adzadalitsa, kuti, Mulungu akuyese iwe monga Efuremu ndi monga Manase; ndipo anaika Efuremu woyamba wa Manase.
Iye wakulandira mneneri, pa dzina la mneneri, adzalandira mphotho ya mneneri; ndipo wakulandira munthu wolungama, pa dzina la munthu wolungama adzalandira mphotho ya munthu wolungama.
Dzina lake lidzakhala kosatha, momwe likhalira dzuwa dzina lake lidzamvekera zidzukulu. Ndipo anthu adzadalitsidwa mwa Iye; amitundu onse adzamutcha wodala.
Pakuti Inu, Mulungu, mudamva zowinda zanga; munandipatsa cholowa cha iwo akuopa dzina lanu.
Potero mwa Iye tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.
Ndinalandira mboni zanu zikhale cholandira chosatha; pakuti ndizo zokondweretsa mtima wanga.
Chifukwa chake ngati munthu aliyense ali mwa Khristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano.
ndipo iwo akudziwa dzina lanu adzakhulupirira Inu; pakuti, Inu Yehova, simunawasiye iwo akufuna Inu.
Ha! Chifundo chanu, Mulungu, nchokondedwadi! Ndipo ana a anthu athawira kumthunzi wa mapiko anu.
ndipo ngati upereka kwa wanjala chimene moyo wako umakhumba, ndi kukhutitsa moyo wovutidwa, pomwepo kuunika kwako kudzauka mumdima, ndipo usiku wako udzanga usana;
Yehova asunga alendo; agwiriziza mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye; koma akhotetsa njira ya oipa.
Ndi mtendere ndidzagona pansi, pomwepo ndidzagona tulo; chifukwa Inu, Yehova, mundikhalitsa ine, ndikhale bwino.
Yehova akudalitse iwe, nakusunge;
Yehova awalitse nkhope yake pa iwe, nakuchitire chisomo;
ndipo Yehova adzakutsogolera posalekai, ndi kukhutitsa moyo wako m'chilala, ndi kulimbitsa mafupa ako; ndipo udzafanana ndi munda wothirira madzi, ndi kasupe wamadzi amene madzi ake saphwa konse.
Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m'zakumwamba mwa Khristu;
Odala iwo amene atsuka miinjiro yao, kuti akakhale nao ulamuliro pa mtengo wa moyo, ndi kuti akalowe m'mzinda pazipata.