Masalimo 23 - Buku LopatulikaAmwai amene Yehova akhala Mbusa wao Salimo la Davide. 1 Yehova ndiye mbusa wanga; sindidzasowa. 2 Andigonetsa kubusa lamsipu, anditsogolera kumadzi odikha. 3 Atsitsimutsa moyo wanga; anditsogolera m'mabande a chilungamo, chifukwa cha dzina lake. 4 Inde, ndingakhale ndiyenda m'chigwa cha mthunzi wa imfa, sindidzaopa choipa; pakuti Inu muli ndi ine; chibonga chanu ndi ndodo yanu, izi zindisangalatsa ine. 5 Mundiyalikira gome pamaso panga m'kuona kwa adani anga; mwandidzoza mutu wanga mafuta; chikho changa chisefuka. 6 Inde ukoma ndi chifundo zidzanditsata masiku onse a moyo wanga, ndipo ndidzakhala m'nyumba ya Yehova masiku onse. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi