Mulungu wandiyang'anira kuyambira ndili m'mimba mwa amayi anga, wanditeteza ku zoipa zonse, wandibisira ku ziwembu za mdani. Ndaona dzanja lake lamphamvu m'moyo wanga, ndipo ndikudziwa kuti ndine cholengedwa chake chamtengo wapatali.
Tsiku lililonse ndimalidza Mulungu chifukwa cha chikondi chake chosatha ndi zabwino zake zosawerengeka. Ndimalimbikitsidwa ndi Mawu ake opatulika, ndipo ndimapeza mtendere mwa Iye. Ngakhale pakati pa mavuto, ndimadziwa kuti Mzimu Woyera ali nane, akundipatsa chitetezo ndi mphamvu.
Palibe chodetsa nkhawa chifukwa ndikudziwa kuti ndili m'manja mwa Wamphamvuyonse. Mulungu wanga, Mpulumutsi wanga, amanditeteza nthawi zonse. Mwa Iye ndimapeza chimwemwe chenicheni ndi mtendere wosatha.
Mphamvu ya Mulungu imandimasula ku ukapolo wa uchimo ndi mantha. Ndimapembedza mwaufulu, wodzazidwa ndi chikondi chake. Ndimadziwa kuti Mulungu amasamalira moyo wanga, akundipatsa mpumulo umene ndimaufuna.
Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe; akapanda kusunga mzinda Yehova, mlonda adikira chabe.
Iye amene akhala pansi m'ngaka yake ya Wam'mwambamwamba adzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse. palibe choipa chidzakugwera, ndipo cholanga sichidzayandikiza hema wako. Pakuti adzalamulira angelo ake za iwe, akusunge m'njira zako zonse. Adzakunyamula pa manja ao, ungagunde phazi lako pamwala. Udzaponda mkango ndi mphiri; udzapondereza msona wa mkango ndi chinjoka. Popeza andikondadi ndidzampulumutsa; ndidzamkweza m'mwamba, popeza adziwa dzina langa. Adzandifuulira Ine ndipo ndidzamyankha; kunsautso ndidzakhala naye pamodzi; ndidzamlanditsa, ndi kumchitira ulemu. Ndidzamkhutitsa ndi masiku ambiri, ndi kumuonetsera chipulumutso changa. Ndidzati kwa Yehova, Pothawirapo panga ndi linga langa; Mulungu wanga, amene ndimkhulupirira.
Ndipo anthu anga adzakhala m'malo a mtendere, ndi mokhala mokhulupirika ndi mopuma mwa phee.
Yehova adzakusunga kukuchotsera zoipa zilizonse; adzasunga moyo wako. Yehova adzasungira kutuluka kwako ndi kulowa kwako, kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.
Inu ndinu mobisalira mwanga; m'nsautso mudzandisunga; mudzandizinga ndi nyimbo za chipulumutso.
Ndipo mau awa ndikuuzani lero, azikhala pamtima panu; ndipo muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m'nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.
Ndipo mwaziwo udzakhala chizindikiro kwa inu pa nyumba zimene mukhalamo; pamene ndiona mwaziwo ndidzapitirira inu, ndipo sipadzakhala mliri wakukuonongani, pakukantha Ine dziko la Ejipito.
Khalani amphamvu, limbikani mitima, musamachita mantha, kapena kuopsedwa chifukwa cha iwowa; popeza Yehova Mulungu wanu ndiye amene amuka nanu; Iye sadzakusowani, kapena kukusiyani.
Kotero kuti tinena molimbika mtima, Mthandizi wanga ndiye Ambuye; sindidzaopa; adzandichitira chiyani munthu?
Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula; ndipo lilime lonse limene lidzakangana nawe m'chiweruzo udzalitsutsa. Ichi ndi cholowa cha atumiki a Yehova, ndi chilungamo chao chimene chifuma kwa Ine, ati Yehova.
Ndi mtendere ndidzagona pansi, pomwepo ndidzagona tulo; chifukwa Inu, Yehova, mundikhalitsa ine, ndikhale bwino.
Ndingakhale ndiyenda pakati pa nsautso, mudzandipatsa moyo; mudzatambasula dzanja lanu pa mkwiyo wa adani anu, ndipo dzanja lanu lamanja lidzandipulumutsa.
ngakhale mpaka mudzakalamba Ine ndine, ndipo ngakhale mpaka tsitsi laimvi, Ine ndidzakusenzani inu; ndalenga, ndipo ndidzanyamula; inde, ndidzasenza, ndipo ndidzapulumutsa.
Mulungu ndiye wangwiro m'njira zake; mau a Yehova ngoyengeka; ndiye chikopa cha onse okhulupirira Iye.
Sudzaopa choopsa cha usiku, kapena muvi wopita usana; kapena mliri woyenda mumdima, kapena chionongeko chakuthera usana.
Koma ine, ndidzaimbira mphamvu yanu; inde ndidzaimbitsa chifundo chanu mamawa, pakuti Inu mwakhala msanje wanga, ndi pothawirapo ine tsiku la nsautso yanga.
Taonani, Ine ndili pamodzi ndi iwe, ndipo ndidzakusunga iwe konse kumene upitako, ndipo ndidzakubwezanso iwe ku dziko lino; chifukwa kuti sindidzakusiya iwe, kufikira kuti nditachita chimene ndanena nawe.
Ambuye adzandilanditsa ku ntchito yonse yoipa, nadzandipulumutsa ine kulowa Ufumu wake wa Kumwamba; kwa Iye ukhale ulemerero kunthawi za nthawi. Amen.
Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa; msanje wanga, sindidzagwedezeka kwakukulu.
usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.
Pakuti kumene kuli awiri kapena atatu asonkhanira m'dzina langa, ndili komweko pakati pao.
Ndipo Inu Yehova, ndinu chikopa changa; ulemerero wanga, ndi wondiweramutsa mutu wanga.
Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu. Kotero kuti tinena molimbika mtima, Mthandizi wanga ndiye Ambuye; sindidzaopa; adzandichitira chiyani munthu?
Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Ndikweza maso anga kumapiri: Thandizo langa lidzera kuti? Thandizo langa lidzera kwa Yehova, wakulenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Inu ndinu ochokera mwa Mulungu, tiana, ndipo munaipambana; pakuti Iye wakukhala mwa inu aposa iye wakukhala m'dziko lapansi. Iwo ndiwo ochokera m'dziko lapansi;
Yehova ndiye kuunika kwanga ndi chipulumutso changa; ndidzaopa yani? Yehova ndiye mphamvu ya moyo wanga; ndidzachita mantha ndi yani?
Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu; pakuti yense wakupempha alandira; ndi wakufunayo apeza; ndi kwa wogogodayo chitsegulidwa.
Iwo akukhulupirira Yehova akunga phiri la Ziyoni, losasunthika, likhazikika kosatha. Monga mapiri azinga Yerusalemu, momwemo Yehova azinga anthu ake, kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.
Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.
Pamene udulitsa pamadzi ndili pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsa; ngakhale lawi silidzakutentha.
Inde, ndingakhale ndiyenda m'chigwa cha mthunzi wa imfa, sindidzaopa choipa; pakuti Inu muli ndi ine; chibonga chanu ndi ndodo yanu, izi zindisangalatsa ine.
Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa chosowa chanu chilichonse monga mwa chuma chake mu ulemerero mwa Khristu Yesu.
Popeza andikondadi ndidzampulumutsa; ndidzamkweza m'mwamba, popeza adziwa dzina langa.
Koma inu, munandipangira ine choipa; koma Mulungu anachipangira chabwino, kuti kuchitike monga lero, kupulumutsa amoyo anthu ambiri.
Koma muyambe mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.
Koma chikhulupiriro ndicho chikhazikitso cha zinthu zoyembekezeka, chiyesero cha zinthu zosapenyeka.
Inu Yehova, simudzandikaniza nsoni zanu, chifundo chanu ndi choonadi chanu zindisunge chisungire.
ndipo Yehova adzakutsogolera posalekai, ndi kukhutitsa moyo wako m'chilala, ndi kulimbitsa mafupa ako; ndipo udzafanana ndi munda wothirira madzi, ndi kasupe wamadzi amene madzi ake saphwa konse.
Khalani chete, ndipo dziwani kuti Ine ndine Mulungu, Ndidzabuka mwa amitundu, ndidzabuka padziko lapansi.
Kodi mpheta ziwiri sizigulidwa kakobiri? Ndipo imodzi ya izo siigwa pansi popanda Atate wanu: Filipo, ndi Bartolomeo; Tomasi, ndi Mateyu wamsonkho yo; Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo; komatu inu, matsitsi onse a m'mutu mwanu awerengedwa. Chifukwa chake musamaopa; inu mupambana mpheta zambiri.
Yembekeza Yehova, limbika, ndipo Iye adzalimbitsa mtima wako; inde, yembekeza Yehova.
M'malo mwa manyazi anu, owirikiza; ndi chitonzo iwo adzakondwera ndi gawo lao; chifukwa chake iwo adzakhala nacho m'dziko mwao cholowa chowirikiza, adzakhala nacho chikondwerero chosatha.
Pakuti mkwiyo wake ukhala kanthawi kokha; koma kuyanja kwake moyo wonse. Kulira kuchezera, koma mamawa kuli kufuula kokondwera.
Popeza tsono tayesedwa olungama ndi chikhulupiriro, tikhala ndi mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu;
Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang'ana iwe.
Ndipo munthu adzakhala monga pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo; monga mitsinje yamadzi m'malo ouma, monga mthunzi wa thanthwe lalikulu m'dziko lotopetsa.
Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse; popeza ali padzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.
Pakuti Mulungu ameneyo ndiye Mulungu wathu kunthawi za nthawi, adzatitsogolera kufikira imfa.
Popeza sadzagwedezeka nthawi zonse; wolungama adzakumbukika ku nthawi yosatha. Sadzaopa mbiri yoipa; mtima wake ngwokhazikika, wokhulupirira Yehova.
ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.
Pondichulukira zolingalira zanga m'kati mwanga, zotonthoza zanu zikondweretsa moyo wanga.
Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.
Mulungu amangitsira banja anthu a pa okha; atulutsa am'ndende alemerere; koma opikisana naye akhala m'dziko lopanda madzi.
Likatha thupi langa ndi mtima wanga, Mulungu ndiye thanthwe la mtima wanga, ndi cholandira changa chosatha.
Yehova adzanditsirizira za kwa ine: Chifundo chanu, Yehova, chifikira kunthawi zonse: Musasiye ntchito za manja anu.
Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso; pokana zimenezi palibe lamulo.
Ndipo uku ndi kulimbika mtima kumene tili nako kwa Iye, kuti ngati tipempha kanthu monga mwa chifuniro chake, atimvera; ndipo ngati tidziwa kuti atimvera chilichonse tichipempha, tidziwa kuti tili nazo izi tazipempha kwa Iye.
Afuule mokondwera nasangalale iwo akukondwera nacho chilungamo changa, ndipo anene kosalekeza, Abuke Yehova, amene akondwera ndi mtendere wa mtumiki wake.
pokhulupirira pamenepo, kuti Iye amene anayamba mwa inu ntchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Khristu;
Koma atero Yehova, Ngakhale am'nsinga a wamphamvu adzalandidwa, ndi chofunkha cha woopsa chidzapulumutsidwa; pakuti Ine ndidzakangana naye amene akangana ndi iwe, ndipo ndidzapulumutsa ana ako.
Pakuti ife ndife alendo pamaso panu, ndi ogonera, monga makolo athu onse; masiku athu a padziko akunga mthunzi, ndipo palibe kukhalitsa.
M'mene ndinasautsika ndinaitanira pa Yehova; anandiyankha nandiika motakasuka Yehova. Yehova ndi wanga; sindidzaopa; adzandichitanji munthu?
Idzani, anthu anga, lowani m'zipinda mwanu, nimutseke pamakomo panu; nimubisale kanthawi kufikira mkwiyo utapita. Pakuti taonani, Yehova adza kuchokera kumalo ake kudzazonda okhala padziko lapansi, chifukwa cha kuipa kwao; dziko lidzavumbulutsa mwazi wake, ndipo silidzavundikiranso ophedwa ake.
Nzeru imangitsa nyumba; luntha liikhazikitsa. Ndinapita pamunda wa waulesi, polima mphesa munthu wosowa nzeru. Taonani, ponsepo panamera minga, ndi kuwirirapo khwisa; tchinga lake lamiyala ndi kupasuka. Pamenepo ndinayang'ana ndi kuganizira, ndinaona ndi kulandira mwambo. Tulo tapang'ono, kungoodzera pang'ono, kungomanga manja pang'ono m'kugona, ndipo umphawi wako udzafika ngati mbala; ndi kusauka kwako ngati munthu wachikopa. Kudziwa kudzaza zipinda zake ndi chuma chonse chofunika cha mtengo wake.
Usaope; pakuti Ine ndili ndi iwe; ndidzatenga mbeu zako kuchokera kum'mawa, ndi kusonkhanitsa iwe kuchokera kumadzulo.
Umsenze Yehova nkhawa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza, nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.
Yehova ndiye wakukusunga; Yehova ndiye mthunzi wako wa kudzanja lako lamanja. Dzuwa silidzawamba usana, mwezi sudzakupanda usiku. Yehova adzakusunga kukuchotsera zoipa zilizonse; adzasunga moyo wako. Yehova adzasungira kutuluka kwako ndi kulowa kwako, kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.
Koma Ambuye ali wokhulupirika amene adzakukhazikitsani inu, nadzakudikirirani kuletsa woipayo;
Potero dzichepetseni pansi padzanja la mphamvu la Mulungu, kuti panthawi yake akakukwezeni; ndi kutaya pa Iye nkhawa yanu yonse, pakuti Iye asamalira inu.