Masalimo 3:3 - Buku Lopatulika3 Ndipo Inu Yehova, ndinu chikopa changa; ulemerero wanga, ndi wondiweramutsa mutu wanga. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Ndipo Inu Yehova, ndinu chikopa changa; ulemerero wanga, ndi wondiweramutsa mutu wanga. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Koma Inu Chauta, ndinu chishango changa chonditeteza, ndinu ulemerero wanga, mumalimbitsa mtima wanga ndinu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Koma Inu Yehova, ndinu chishango chonditeteza, Inu mwandiveka ulemerero ndipo mwanditukula. Onani mutuwo |
Ndipo kunali chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi ziwiri cha kumtenga ndende Yehoyakini mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi ndi ziwiri, tsiku la makumi awiri mphambu asanu ndi awiri la mwezi, Evili-Merodaki mfumu ya Babiloni anamuweramutsa mutu wake wa Yehoyakini mfumu ya Yuda atuluke m'kaidi, chaka cholowa iye ufumu wake;