Masalimo 3:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Koma Inu Yehova, ndinu chishango chonditeteza, Inu mwandiveka ulemerero ndipo mwanditukula. Onani mutuwoBuku Lopatulika3 Ndipo Inu Yehova, ndinu chikopa changa; ulemerero wanga, ndi wondiweramutsa mutu wanga. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Ndipo Inu Yehova, ndinu chikopa changa; ulemerero wanga, ndi wondiweramutsa mutu wanga. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Koma Inu Chauta, ndinu chishango changa chonditeteza, ndinu ulemerero wanga, mumalimbitsa mtima wanga ndinu. Onani mutuwo |
mpaka nditabwera kudzakutengani kupita ku dziko lofanana ndi lanuli, dziko la tirigu ndi vinyo watsopano, dziko la chakudya ndi minda ya mipesa, dziko la mitengo ya olivi ndi uchi. Sankhani moyo osati imfa! “Musamvere zonena Hezekiya, pakuti iye akukusocheretsani ponena kuti, ‘Yehova adzatipulumutsa.’