Masalimo 3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa ChaleroSalimo 3 Salimo la Davide. Atathawa mwana wake Abisalomu. 1 Inu Yehova, achulukadi adani anga! Achulukadi amene andiwukira! 2 Ambiri akunena za ine kuti, “Mulungu sadzamupulumutsa.” Sela 3 Koma Inu Yehova, ndinu chishango chonditeteza, Inu mwandiveka ulemerero ndipo mwanditukula. 4 Kwa Yehova, Ine ndilira mofuwula ndipo Iye amandiyankha kuchokera ku phiri lake loyera. Sela 5 Ine ndimagona ndi kupeza tulo; ndimadzukanso chifukwa Yehova amandichirikiza. 6 Sindidzaopa adani anga osawerengeka amene abwera kulimbana nane kuchokera ku madera onse. 7 Dzukani, Inu Yehova! Pulumutseni, Inu Mulungu wanga. Akantheni adani anga onse pa msagwada; gululani mano a anthu oyipa. 8 Chipulumutso chimachokera kwa Yehova. Madalitso akhale pa anthu anu. Sela |
The Word of God in Contemporary Chichewa
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.®
Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.®
Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.
Biblica, Inc.