Masalimo 3 - Buku LopatulikaKukhulupirika kwa Mulungu Salimo la Davide, muja anathawa Abisalomu mwana wake. 1 Yehova! Ha! Achuluka nanga akundisautsa ine! Akundiukira ine ndi ambiri. 2 Ambiri amati kwa moyo wanga, alibe chipulumutso mwa Mulungu. 3 Ndipo Inu Yehova, ndinu chikopa changa; ulemerero wanga, ndi wondiweramutsa mutu wanga. 4 Ndifuula kwa Yehova ndi mau anga, ndipo andiyankha m'phiri lake loyera. 5 Ndinagona ine pansi, ndinagona tulo; ndinauka; pakuti Yehova anandichirikiza. 6 Sindidzaopa unyinji wa anthu akundizinga ine. 7 Ukani Yehova; ndipulumutseni, Mulungu wanga! Pakuti mwapanda adani anga onse patsaya; mwawathyola mano oipawo. 8 Chipulumutso ncha Yehova; dalitso lanu likhale pa anthu anu. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi