Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 3:4 - Buku Lopatulika

4 Ndifuula kwa Yehova ndi mau anga, ndipo andiyankha m'phiri lake loyera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndifuula kwa Yehova ndi mau anga, ndipo andiyankha m'phiri lake loyera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Ndimafuulira Chauta kuti andithandize, Iye amandiyankha ali pa phiri lake loyera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Kwa Yehova, Ine ndilira mofuwula ndipo Iye amandiyankha kuchokera ku phiri lake loyera. Sela

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 3:4
29 Mawu Ofanana  

Zitapita izo, mau a Yehova anadza kwa Abramu m'masomphenya, kuti, Usaope, Abramu, Ine ndine chikopa chako ndi mphotho yako yaikulukulu.


Inu ndinu pobisalapo panga, ndi chikopa changa; ndiyembekezera mau anu.


Tsiku loitana ine, munandiyankha, munandilimbitsa ndi mphamvu m'moyo mwanga.


Ndidzaitanira Yehova, woyenera kutamandika, ndipo adzandipulumutsa ine kwa adani anga.


Koma Ine ndadzoza mfumu yanga Pa Ziyoni, phiri langa loyera.


Ndipo tsopano mutu wanga udzakwezeka pamwamba pa adani anga akundizinga; ndipo ndidzapereka m'chihema mwake nsembe za kufuula mokondwera; ndidzaimba, inde, ndidzaimbira Yehova zomlemekeza.


Yehova ndiye mphamvu yanga, ndi chikopa changa; mtima wanga wakhulupirira Iye, ndipo anandithandiza, chifukwa chake mtima wanga ukondwera kwakukulu; ndipo ndidzamyamika nayo nyimbo yanga.


Ndinafuna Yehova ndipo anandivomera, nandilanditsa m'mantha anga onse.


Munthu uyu wozunzika anafuula, ndipo Yehova anamumva, nampulumutsa m'masautso ake onse.


Tumizirani kuunika kwanu ndi choonadi chanu zinditsogolere; zindifikitse kuphiri lanu loyera, kumene mukhala Inuko.


Ndipo undiitane tsiku la chisautso, ndidzakulanditsa, ndipo iwe udzandilemekeza.


Khulupirirani pa Iye nyengo zonse, anthu inu, tsanulirani mitima yanu pamaso pake. Mulungu ndiye pothawirapo ife.


Yehova wa makamu, wodala munthu wakukhulupirira Inu.


Pamenepo munalankhula m'masomphenya ndi okondedwa anu, ndipo mudati, Ndasenza thandizo pa chiphona; ndakweza wina wosankhika mwa anthu.


Adzandifuulira Ine ndipo ndidzamyankha; kunsautso ndidzakhala naye pamodzi; ndidzamlanditsa, ndi kumchitira ulemu.


Mkwezeni Yehova Mulungu wathu, ndipo gwadirani paphiri lake loyera; pakuti Yehova Mulungu wathu ndiye woyera.


Iye asungira oongoka mtima nzeru yeniyeni; ndiye chikopa cha oyenda molunjika;


Ndipo padzakhala kuti iwo asanaitane Ine, ndidzayankha; ndipo ali chilankhulire, Ine ndidzamva.


munamva mau anga; musabise khutu lanu popuma ndi pofuula ine.


Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu;


Kodi wina wa inu akumva zowawa? Apemphere. Kodi wina asekera? Aimbire.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa