Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 3:7 - Buku Lopatulika

7 Ukani Yehova; ndipulumutseni, Mulungu wanga! Pakuti mwapanda adani anga onse patsaya; mwawathyola mano oipawo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ukani Yehova; ndipulumutseni, Mulungu wanga! Pakuti mwapanda adani anga onse patsaya; mwawathyola mano oipawo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Inu Chauta, dzambatukani, mundipulumutse Inu Mulungu wanga. Adani anga onse mwaŵaomba makofi, anthu oipa mwaŵagulula mano.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Dzukani, Inu Yehova! Pulumutseni, Inu Mulungu wanga. Akantheni adani anga onse pa msagwada; gululani mano a anthu oyipa.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 3:7
17 Mawu Ofanana  

Pakuti nkhondo inatanda padziko lonse, ndipo tsiku lomwelo nkhalango inaononga anthu akuposa amene anaonongeka ndi lupanga.


Iwo anandiyasamira pakamwa pao; anandiomba pama ndi kunditonza; asonkhana pamodzi kunditsutsa.


Ndipo ndinathyola nsagwada ya wosalungama, ndi kukwatula chogwidwa kumano kwake.


Ukani, Yehova; samulani dzanja lanu, Mulungu; musaiwale ozunzika.


Chifukwa cha kupasuka kwa ozunzika, chifukwa cha kuusa moyo kwa aumphawi, ndiuka tsopano, ati Yehova; ndidzamlonga mosungika muja alakalakamo.


Lingakhale gulu la ankhondo limanga misasa kuti andithyole, mtima wanga sungachite mantha; ingakhale nkhondo ikandiukira, inde pomweponso ndidzakhulupirira.


Galamukani, ndipo khalani maso kundiweruzira mlandu wanga, Mulungu wanga ndi Ambuye wanga.


Galamukani, mugoneranji, Ambuye? Ukani, musatitaye chitayire.


Thyolani mano ao m'kamwa mwao, Mulungu, zulani zitsakano za misona ya mkango, Yehova.


Ndinu Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israele. Ukani kukazonda amitundu onse, musachitire chifundo mmodzi yense wakuchita zopanda pake monyenga.


Bwererani Yehova, landitsani moyo wanga; ndipulumutseni chifukwa cha kukoma mtima kwanu.


Ukani Yehova mu mkwiyo wanu, nyamukani chifukwa cha ukali wa akundisautsa; ndipo mugalamukire ine; mwalamulira chiweruzo.


Mubwezeranji dzanja lanu, ndilo dzanja lamanja lanu? Mulitulutse kuchifuwa chanu ndipo muwatheretu.


pakuuka Mulungu kuti aweruze, kuti apulumutse ofatsa onse a padziko lapansi.


Galamuka, galamuka, khala ndi mphamvu, mkono wa Yehova; galamuka monga masiku akale, mibadwo ya nthawi zakale. Kodi si ndiwe amene unadula Rahabu zipinjirizipinjiri; amene unapyoza chinjoka chamnyanja chija?


Atembenuzire wompanda tsaya lake, adzazidwe ndi chitonzo.


Tsoka iye wakunena kwa mtengo, Galamuka; ndi kwa mwala wosalankhula, Nyamuka! Kodi ichi chiphunzitsa? Taona chakutidwa ndi golide ndi siliva, ndi m'kati mwake mulibe mpweya konse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa