Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 46:10 - Buku Lopatulika

10 Khalani chete, ndipo dziwani kuti Ine ndine Mulungu, Ndidzabuka mwa amitundu, ndidzabuka padziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Khalani chete, ndipo dziwani kuti Ine ndine Mulungu, Ndidzabuka mwa amitundu, ndidzabuka pa dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 “Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Iye akuti, “Khala chete, ndipo dziwa kuti ndine Mulungu; ndidzakwezedwa pakati pa mitundu ya anthu; ine ndidzakwezedwa mʼdziko lapansi.”

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 46:10
26 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali, nthawi ya kupereka nsembe yamadzulo, Eliya mneneri anasendera, nati, Yehova Mulungu wa Abrahamu ndi Isaki ndi Israele, lero kudziwike kuti Inu ndinu Mulungu wa Israele, ndi ine mtumiki wanu, kuti mwa mau anu ndachita zonsezi.


Kodi milungu ya amitundu inawalanditsa amene makolo anga anawaononga, ndiwo Gozani, ndi Harani Rezefe, ndi ana a Edeni okhala mu Telasara?


Ndipo anawakonzera chakudya chambiri, nadya namwa iwo; nawauza amuke; namuka kwa mbuye wao. Ndipo magulu a Aramu sanadzenso ku dziko la Israele.


Ukulu, ndi mphamvu, ndi ulemerero, ndi chipambano, ndi chifumu ndi zanu, Yehova; pakuti zonse zam'mwamba ndi padziko lapansi ndi zanu; ufumu ndi wanu, Yehova; ndipo mwakwezeka mutu wa pa zonse.


Dziwani kuti Yehova ndiye Mulungu; Iyeyu anatilenga, ndipo ife ndife ake; ndife anthu ake ndi nkhosa zapabusa pake.


Kwezekani, Yehova, mu mphamvu yanu; potero tidzaimba ndi kulemekeza chilimbiko chanu.


Lupanga lao lidzalowa m'mtima mwao momwe, ndipo mauta ao adzathyoledwa.


Mukwezeke m'mwambamwamba, Mulungu; ulemerero wanu ukhale pamwamba padziko lonse lapansi.


Kuti adziwe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu Wam'mwambamwamba padziko lonse lapansi.


Tsopano ndidziwa kuti Yehova ali wamkulu ndi milungu yonse, pakuti momwe anadzikuza okha momwemo anawaposa.


Maso a munthu akuyang'anira kumwamba adzatsitsidwa, ndi kudzikweza kwa anthu kudzaweramitsidwa pansi; ndipo Yehova yekha adzakwezedwa tsiku limenelo.


Ndipo kudzikweza kwa munthu kudzaweramitsidwa pansi, kudzikuza kwa munthu kudzatsitsidwa; ndipo Yehova yekha adzakwezedwa tsiku limenelo.


Iye adzaweruza pakati pa akunja, adzadzudzula mitundu yambiri ya anthu; ndipo iwo adzasula malupanga ao akhale zolimira, ndi nthungo zao zikhale makasu; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.


koma Yehova wa makamu wakwezedwa m'chiweruziro, ndipo Mulungu Woyera wayeretsedwa m'chilungamo.


Yehova wa makamu atero: Taonani, ndidzathyola uta wa Elamu, ndiwo mtima wa mphamvu yao.


Ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, nditaika moto mu Ejipito, naonongeka onse akumthandiza.


Momwemo ndidzadzikuzitsa, ndi kudzizindikiritsa woyera, ndipo ndidzadziwika pamaso pa amitundu ambiri; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.


ndipo ndidzakantha uta wako kuuchotsa m'dzanja lako lamanzere, ndi kutayitsa mivi yako kudzanja lako lamanja.


Ndipo Iye adzaweruza mwa mitundu yambiri ya anthu, nadzadzudzula amitundu amphamvu ali kutali; ndipo iwo adzasula malupanga ao akhale makasu, ndi mikondo yao ikhale zolimira, mtundu wa anthu sudzasamulira mtundu unzake lupanga, kapena kuphunziranso nkhondo.


Koma Yehova ali mu Kachisi wake wopatulika; dziko lonse lapansi likhale chete pamaso pake.


Khalani chete, anthu onse, pamaso pa Yehova; pakuti wagalamuka mokhalira mwake mopatulika.


Koma Yehova anati kwa Yoswa, Usaope chifukwa cha iwowa; pakuti mawa, dzuwa lino ndidzawapereka onse ophedwa pamaso pa Israele; udzawadula mitsindo akavalo ao, ndi kutentha agaleta ao ndi moto.


Ndipo Yoswa anawachitira monga Yehova adamuuza: nadula akavalo ao mitsindo, natentha magaleta ao ndi moto.


Lero lino Yehova adzakupereka iwe m'dzanja langa, ndipo ndidzakukantha, ndi kukuchotsera mutu wako. Ndipo lero ndidzapatsa mitembo ya makamu a Afilisti kwa mbalame za mlengalenga, ndi kwa zilombo za dziko lapansi; kuti dziko lonse likazindikire kuti kwa Israele kuli Mulungu.


Mauta a amphamvu anathyoka, koma okhumudwawo amangiridwa ndi mphamvu m'chuuno.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa