2 Timoteyo 4:18 - Buku Lopatulika18 Ambuye adzandilanditsa ku ntchito yonse yoipa, nadzandipulumutsa ine kulowa Ufumu wake wa Kumwamba; kwa Iye ukhale ulemerero kunthawi za nthawi. Amen. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201418 Ambuye adzandilanditsa ku ntchito yonse yoipa, nadzandipulumutsa ine kulowa Ufumu wake wa Kumwamba; kwa Iye ukhale ulemerero kunthawi za nthawi. Amen. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa18 Ambuye adzandipulumutsanso ku chilichonse chofuna kundichita choipa, ndipo adzandisunga bwino mpaka kundiloŵetsa mu Ufumu wake wa Kumwamba. Kwa Iye kukhale ulemerero kwamuyaya. Amen. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero18 Ambuye adzandilanditsa ku chilichonse chofuna kundichita choyipa ndipo adzandisamalira bwino mpaka kundilowetsa chonse mu ufumu wake wakumwamba. Kwa Iye kukhale ulemerero mpaka muyaya. Onani mutuwo |
Ndipo pamene Davide anamva kuti Nabala adamwalira, iye anati, Alemekezedwe Yehova, amene anaweruza mlandu wa mtonzo wanga wochokera ku dzanja la Nabala, naletsa mnyamata wake pa choipa; ndipo Yehova anabwezera pamutu pa Nabala choipa chake. Ndipo Davide anatumiza wokamfunsira Abigaile, zakuti amtengere akhale mkazi wake.