Masalimo 51 - Buku LopatulikaDavide avomereza kuchimwa kwake, apempha Mulungu amkhululukire, asamchotsere Mzimu Woyera Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide; m'mene anamdzera Natani mneneriyo atalowa iye kwa Bateseba. 1 Mundichitire ine chifundo, Mulungu, monga mwa kukoma mtima kwanu; monga mwa unyinji wa nsoni zanu zokoma mufafanize machimo anga. 2 Mubwereze kunditsuka mphulupulu yanga, ndipo mundiyeretse kundichotsera choipa changa. 3 Chifukwa ndazindikira machimo anga; ndipo choipa changa chili pamaso panga chikhalire. 4 Pa Inu, Inu nokha, ndinachimwa, ndipo ndinachichita choipacho pamaso panu; kuti mukhale wolungama pakulankhula Inu, mukhalenso woyera pa kuweruza kwanu. 5 Onani, ndinabadwa m'mphulupulu, ndipo mai wanga anandilandira m'zoipa. 6 Onani, Inu mukondwera ndi zoonadi m'malo a m'katimo; ndipo m'malo a m'tseri mudzandidziwitsa nzeru. 7 Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera; munditsuke ndipo ndidzakhala wa mbuu woposa matalala. 8 Mundimvetse chimwemwe ndi kusekera, kuti mafupawo munawathyola akondwere. 9 Muzibisire nkhope yanu zolakwa zanga, ndipo mufafanize mphulupulu zanga zonse. 10 Mundilengere mtima woyera, Mulungu; mukonze mzimu wokhazikika m'kati mwanga. 11 Musanditaye kundichotsa pamaso panu; musandichotsere Mzimu wanu Woyera. 12 Mundibwezere chimwemwe cha chipulumutso chanu; ndipo mzimu wakulola undigwirizize. 13 Pomwepo ndidzalangiza ochimwa njira zanu; ndipo olakwa adzabwera kwa Inu. 14 Mundilanditse kumlandu wa mwazi, Mulungu, ndinu Mulungu wa chipulumutso changa; lilime langa lidzakweza nyimbo ya chilungamo chanu. 15 Ambuye, tsegulani pa milomo yanga; ndipo pakamwa panga padzalalikira ulemekezo wanu. 16 Pakuti simukondwera ndi nsembe, mwenzi nditapereka; nsembe yopsereza simuikonda. 17 Nsembe za Mulungu ndizo mzimu wosweka; Inu, Mulungu, simudzaupeputsa mtima wosweka ndi wolapa. 18 Chitirani Ziyoni chokoma monga mwa kukondwera kwanu; mumange malinga a miyala a Yerusalemu. 19 Pamenepo mudzakondwera nazo nsembe zachilungamo, ndi nsembe yopsereza ndi yopsereza yathunthu; pamenepo adzapereka ng'ombe paguwa lanu la nsembe. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi