Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 51:3 - Buku Lopatulika

3 Chifukwa ndazindikira machimo anga; ndipo choipa changa chili pamaso panga chikhalire.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Chifukwa ndazindikira machimo anga; ndipo choipa changa chili pamaso panga chikhalire.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Zolakwa zanga ndikuzidziŵa, kuchimwa kwanga ndikukuzindikira nthaŵi zonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Pakuti ndikudziwa mphulupulu zanga, ndipo tchimo langa lili pamaso panga nthawi zonse.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 51:3
12 Mawu Ofanana  

Nadzipatula a mbumba ya Israele kwa alendo onse, naimirira, nawulula zochimwa zao, ndi mphulupulu za makolo ao.


Apenyerera anthu, ndi kuti, ndinachimwa, ndaipsa choongokacho, ndipo sindinapindule nako.


Ndinavomera choipa changa kwa Inu; ndipo mphulupulu yanga sindinaibise. Ndinati, Ndidzaululira Yehova machimo anga; ndipo munakhululukira choipa cha kulakwa kwanga.


Pakuti ndidzafotokozera mphulupulu yanga; nditenga nkhawa chifukwa cha tchimo langa.


Pakuti zoipa zosawerengeka zandizinga, zochimwa zanga zandipeza kotero kuti sindikhoza kupenya; ziposa tsitsi la mutu wanga, ndipo wandichokera mtima.


Adani anga andinenera choipa, ndi kuti, adzafa liti, ndi kutayika dzina lake?


Wobisa machimo ake sadzaona mwai; koma wakuwavomereza, nawasiya adzachitidwa chifundo.


Ine, Inedi, ndine amene ndifafaniza zolakwa zako, chifukwa cha Ine mwini; ndipo Ine sindidzakumbukira machimo ako.


Pakuti zolakwa zathu zachuluka pamaso pa Inu, ndipo machimo athu atineneza ife; pakuti zolakwa zathu zili ndi ife, ndipo zoipa zathu tizidziwa;


Tigone m'manyazi athu, kunyala kwathu kutifunde ife; pakuti tamchimwira Yehova Mulungu wathu, ife ndi makolo athu, kuyambira ubwana wathu kufikira lero lomwe; ndipo sitidamvere mau a Yehova Mulungu wathu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa