Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 51:14 - Buku Lopatulika

14 Mundilanditse kumlandu wa mwazi, Mulungu, ndinu Mulungu wa chipulumutso changa; lilime langa lidzakweza nyimbo ya chilungamo chanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Mundilanditse kumlandu wa mwazi, Mulungu, ndinu Mulungu wa chipulumutso changa; lilime langa lidzakweza nyimbo ya chilungamo chanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Mundikhululukire mlandu wanga wokhetsa magazi, Inu Mulungu, Mulungu Mpulumutsi wanga, ndipo ndidzakweza mau poimba za chipulumutso chanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Mundipulumutse ku tchimo lokhetsa magazi, Inu Mulungu, Mulungu wa chipulumutso changa, ndipo lilime langa lidzayimba zachilungamo chanu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 51:14
27 Mawu Ofanana  

Ndipo Rubeni anayankha nati kwa iwo, Kodi sindinanene kwa inu kuti, Musachimwire mwanayu; ndipo inu munakana kumvera? Chifukwa chakenso, taonani mwazi wake ufunidwa.


Amene akhetsa mwazi wa munthu, ndi munthunso mwazi wake udzakhetsedwa: chifukwa m'chifanizo cha Mulungu Iye anampanga munthu.


Chifukwa ninji unapeputsa mau a Yehova ndi kuchita chimene chili choipa pamaso pake? Unakantha Uriya Muhiti ndi lupanga ndi kutenga mkazi wake akhale mkazi wako; ndipo unamupha iye ndi lupanga la ana a Amoni.


Ndipo m'masiku a Davide munali njala, zaka zitatu; ndipo Davide anafunsira kwa Yehova. Ndipo Yehova anati, Ndicho chifukwa cha Saulo ndi nyumba yake yamwazi, popeza iye anawapha Agibiyoni.


Ndipo pambuyo pake, pakuchimva Davide, anati, Ine ndi ufumu wanga tikhala osachimwira mwazi wa Abinere mwana wa Nere, nthawi zonse, pamaso pa Yehova;


Ndipo zitatigwera zonsezi chifukwa cha ntchito zathu zoipa ndi kupalamula kwathu kwakukulu; popeza inu Mulungu wathu mwatilanga motichepsera mphulupulu zathu, ndi kutipatsa chipulumutso chotere;


Koma Inu ndinu wolungama mwa zonse zatigwera; pakuti mwachita zoona, koma ife tachita choipa;


Munditsogolere m'choonadi chanu, ndipo mundiphunzitse; pakuti Inu ndinu Mulungu wa chipulumutso changa; Inu ndikuyembekezerani tsiku lonseli.


Musandichotsere mzimu wanga pamodzi ndi olakwa, kapena moyo wanga pamodzi ndi anthu okhetsa mwazi;


Ndipo lilime langa lilalikire chilungamo chanu, ndi lemekezo lanu tsiku lonse.


Fulumirani kundithandiza, Ambuye, chipulumutso changa.


Koma Inu, Mulungu, mudzawatsitsira kudzenje la chionongeko. Anthu okhetsa mwazi ndi achinyengo masiku ao sadzafikira nusu; koma ine ndidzakhulupirira Inu.


Mulungu akhala kwa ife Mulungu wa chipulumutso; ndipo Yehova Ambuye ali nazo zopulumutsira kuimfa.


Yehova, Mulungu wa chipulumutso changa, ndinafuula pamaso panu usana ndi usiku.


Taonani, Mulungu ndiye chipulumutso changa; ndidzakhulupirira, sindidzaopa; pakuti Yehova Mwini ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, Iye ndiye chipulumutso changa.


Koma Israele adzapulumutsidwa ndi Yehova ndi chipulumutso chosatha; inu simudzakhala ndi manyazi, pena kuthedwa nzeru kunthawi zosatha.


Ndikati Ine kwa woipa, Woipawe, udzafa ndithu, osanena iwe kumchenjeza woipayo aleke njira yake, woipa uyo adzafa m'mphulupulu yake, koma mwazi wake ndidzaufunsa padzanja lako.


Ambuye, monga mwa chilungamo chanu chonse, mkwiyo wanu ndi ukali wanu zitembenuketu, zichoke kumzinda wanu Yerusalemu, phiri lanu lopatulika; pakuti mwa zochimwa zathu, ndi mphulupulu za makolo athu, Yerusalemu ndi anthu anu asanduka chotonza cha onse otizungulira.


Ambuye, chilungamo ncha Inu, koma kwa ife manyazi a nkhope yathu, monga lero lino; kwa anthu a Yuda, ndi kwa okhala mu Yerusalemu, ndi kwa Aisraele onse okhala pafupi ndi okhala kutali, kumaiko onse kumene mudawaingira, chifukwa cha kulakwa kwao anakulakwirani nako.


Koma kulumbira, ndi kunama, ndi kupha, ndi kuba, ndi kuchita chigololo; aboola, ndi mwazi ukhudzana nao mwazi.


koma ndidzakondwera mwa Yehova, ndidzasekerera mwa Mulungu wa chipulumutso changa.


Koma pamene iwo, anamkana, nachita mwano, anakutumula malaya ake, nati kwa iwo, Mwazi wanu ukhale pa mitu yanu; ine ndilibe kanthu; kuyambira tsopano ndinka kwa amitundu.


Chifukwa chake ndikuchitirani umboni lero lomwe, kuti ndilibe kanthu ndi mwazi wa anthu onse.


Pakuti pakusadziwa chilungamo cha Mulungu, ndipo pofuna kukhazikitsa chilungamo cha iwo okha, iwo sanagonje ku chilungamo cha Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa