Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 51:1 - Buku Lopatulika

1 Mundichitire ine chifundo, Mulungu, monga mwa kukoma mtima kwanu; monga mwa unyinji wa nsoni zanu zokoma mufafanize machimo anga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Mundichitire ine chifundo, Mulungu, monga mwa kukoma mtima kwanu; monga mwa unyinji wa nsoni zokoma zanu mufafanize machimo anga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Mundichitire chifundo, Inu Mulungu, malinga ndi chikondi chanu chosasinthika. Mufafanize machimo anga, malinga ndi chifundo chanu chachikulu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mundichitire chifundo, Inu Mulungu, molingana ndi chikondi chanu chosasinthika; molingana ndi chifundo chanu chachikulu mufafanize mphulupulu zanga.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 51:1
31 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali pa madzulo Davide anauka pa kama wake nayenda pa tsindwi la nyumba ya mfumu. Ndipo iye ali patsindwipo anaona mkazi alinkusamba; ndi mkaziyo anali wochititsa kaso pomuyang'ana.


ndipo musakwirira mphulupulu yao, ndi kulakwa kwao kusafafanizike pamaso panu; pakuti anautsa mkwiyo wanu pamaso pa omanga linga.


Ndipo anawakumbukira chipangano chake, naleza monga mwa kuchuluka kwa chifundo chake.


Makolo athu sanadziwitse zodabwitsa zanu mu Ejipito; sanakumbukire zachifundo zanu zaunyinji; koma anapikisana ndi Inu kunyanja, ku Nyanja Yofiira.


Koma Inu, Yehova Ambuye, muchite nane chifukwa cha dzina lanu; ndilanditseni popeza chifundo chanu ndi chabwino.


Muchitire mtumiki wanu monga mwa chifundo chanu, ndipo ndiphunzitseni malemba anu.


Yehova achitira chokoma onse; ndi nsoni zokoma zake zigwera ntchito zake zonse.


Pakufuula ine mundiyankhe, Mulungu wa chilungamo changa; pondichepera mwandikulitsira malo. Ndichitireni chifundo, imvani pemphero langa.


Inu Yehova, simudzandikaniza nsoni zanu, chifundo chanu ndi choonadi chanu zindisunge chisungire.


Koma ine, mwa kuchuluka kwa chifundo chanu ndidzalowa m'nyumba yanu; ndidzagwada kuyang'ana Kachisi wanu woyera ndi kuopa Inu.


Muzibisire nkhope yanu zolakwa zanga, ndipo mufafanize mphulupulu zanga zonse.


Koma ine, pemphero langa lili kwa Inu, Yehova, m'nyengo yolandirika; Mulungu, mwa chifundo chanu chachikulu, mundivomereze ndi choonadi cha chipulumutso chanu.


Mundiyankhe Yehova; pakuti chifundo chanu nchokoma; munditembenukire monga mwa unyinji wa nsoni zokoma zanu.


Kodi Mulungu waiwala kuchita chifundo? Watsekereza kodi nsoni zokoma zake mumkwiyo?


Ine, Inedi, ndine amene ndifafaniza zolakwa zako, chifukwa cha Ine mwini; ndipo Ine sindidzakumbukira machimo ako.


Ine ndafafaniza monga mtambo wochindikira zolakwa zako, ndi monga mtambo machimo ako; bwerera kwa Ine, pakuti ndakuombola.


Tayang'anani kunsi kuchokera kumwamba, taonani pokhala panu poyera, ndi pa ulemerero wanu, changu chanu ndi ntchito zanu zamphamvu zili kuti? Mwanditsekerezera zofunafuna za mtima wanu ndi chisoni chanu.


Ndidzatchula zachifundo chake cha Yehova, ndi matamando a Yehova, monga mwa zonse zimene Yehova wapereka kwa ife; ndi ubwino wake waukulu kwa banja la Israele, umene Iye wapereka kwa iwo, monga mwa chifundo chake, ndi monga mwa ntchito zochuluka za chikondi chake.


Koma, Yehova, mudziwa uphungu wao wonse wakundinenera ine kundipha ine; musakhulukire mphulupulu yao, musafafanize tchimo lao pamaso panu; aphunthwitsidwe pamaso panu; muchite nao m'nthawi ya mkwiyo wanu.


Angakhale aliritsa, koma adzachitira chisoni monga mwa kuchuluka kwa zifundo zake.


Mulungu wanga, tcherani khutu, nimumvere, tsegulani maso anu, nimupenye zopasuka zathu, ndi mzinda udatchedwawo dzina lanu; pakuti dzina lanu; pakuti sititula mapembedzero athu pamaso panu, chifukwa cha ntchito zathu zolungama, koma chifukwa cha zifundo zanu zochuluka.


Ambuye Mulungu wathu ndiye wachifundo, ndi wokhululukira; pakuti tampandukira Iye;


Chifukwa chake lapani, bwererani kuti afafanizidwe machimo anu, kotero kuti zidze nyengo zakutsitsimutsa zochokera kunkhope ya Ambuye;


adatha kutifafanizira cha pa ifecho cholembedwa m'zoikikazo, chimene chinali chotsutsana nafe: ndipo anachichotsera pakatipo, ndi kuchikhomera ichi pamtanda;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa