Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -

Masalimo 113 - Buku Lopatulika


Anthu onse alemekeze dzina la Mulungu wothandiza aumphawi

1 Aleluya; Lemekezani, inu atumiki a Yehova; lemekezani dzina la Yehova.

2 Lodala dzina la Yehova Kuyambira tsopano kufikira kosatha.

3 Chitulukire dzuwa kufikira kulowa kwake lilemekezedwe dzina la Yehova.

4 Yehova akwezeka pamwamba pa amitundu onse, ulemerero wake pamwambamwamba.

5 Akunga Yehova Mulungu wathu ndani? Amene akhala pamwamba patali,

6 nadzichepetsa apenye zam'mwamba ndi za padziko lapansi.

7 Amene autsa wosauka kumchotsa kufumbi, nakweza waumphawi kumchotsa kudzala.

8 Kuti amkhalitse pamodzi ndi akulu, pamodzi ndi akulu a anthu ake.

9 Asungitsa nyumba mkazi wosaona mwana, akhale mai wokondwera ndi ana. Aleluya.

Bible Society of Malawi

Bible Society of Malawi
Titsatireni:



Zotsatsa