Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 113:4 - Buku Lopatulika

4 Yehova akwezeka pamwamba pa amitundu onse, ulemerero wake pamwambamwamba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Yehova akwezeka pamwamba pa amitundu onse, ulemerero wake pamwambamwamba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Chauta akulamulira anthu a mitundu yonse, ulemerero wake ndi waukulu kuposa wa mlengalenga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Yehova wakwezeka pa anthu a mitundu yonse, ulemerero wake ndi woposa mayiko akumwamba.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 113:4
10 Mawu Ofanana  

Kodi Mulungu adzakhala ndithu padziko lapansi? Taonani, thambo ndi mu Mwambamwamba zichepa kukulandirani, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimangayi.


Alemekeze dzina la Yehova; pakuti dzina lake lokha ndi lokwezeka; ulemerero wake uli pamwamba padziko lapansi ndi thambo.


Yehova, Ambuye wathu, dzina lanu liposadi nanga padziko lonse lapansi! Inu amene munaika ulemerero wanu pa thambo la kumwamba.


Pakuti Inu, Yehova, ndinu Wam'mwambamwamba padziko lonse lapansi, ndinu wokwezeka kwakukulu pamwamba pa milungu ina yonse.


Yehova ndiye wamkulu mu Ziyoni; ndipo akwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.


Taonani, amitundu akunga dontho la m'mtsuko, nawerengedwa ngati fumbi losalala la m'muyeso; taonani atukula zisumbu ngati kanthu kakang'ono.


Amitundu onse ali chabe pamaso pa Iye; awayesa ngati chinthu chachabe, ndi chopanda pake.


Ndi Iye amene akhala pamwamba pa malekezero a dziko lapansi, ndipo okhalamo akunga ziwala; amene afutukula thambo ngati chinsalu, naliyala monga hema wakukhalamo;


Atero Yehova, Kumwamba ndi mpando wanga wachifumu, ndi dziko lapansi ndi choikapo mapazi anga; mudzandimangira Ine nyumba yotani? Ndi malo ondiyenera kupumamo ali kuti?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa