Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 113:6 - Buku Lopatulika

6 nadzichepetsa apenye zam'mwamba ndi za padziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 nadzichepetsa apenye zam'mwamba ndi za pa dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 wochita kuŵeramira pansi poyang'ana mlengalenga ndi dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 amene amawerama pansi kuyangʼana miyamba ndi dziko lapansi?

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 113:6
9 Mawu Ofanana  

Taona, Mulungu sakhulupirira opatulika ake; ngakhale m'mwamba simuyera pamaso pake.


Pakuti apenyerera malekezero a dziko lapansi, naona pansi pa thambo ponse;


Taona, sakhulupirira atumiki ake; nawanenera amithenga ake zopusa;


Yehova ali mu Kachisi wake woyera, Yehova, mpando wachifumu wake uli mu Mwamba; apenyerera ndi maso ake, ayesa ana a anthu ndi zikope zake.


Angakhale Yehova ngwokwezeka, apenyanso wopepukayo; koma wodzikuza amdziwira kutali.


M'malo akhalamo Iye, amapenya pansi pa onse akukhala m'dziko lapansi.


Pakuti atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m'malo aatali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.


Pamwamba pa Iye panaima aserafi; yense anali ndi mapiko asanu ndi limodzi; awiri anaphimba nao nkhope yake, awiri naphimba nao mapazi ake, awiri nauluka nao.


Pakuti zonsezi mkono wanga wazilenga, momwemo zonsezi zinaoneka, ati Yehova; koma ndidzayang'anira munthu uyu amene ali waumphawi, ndi wa mzimu wosweka, nanthunthumira ndi mau anga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa