Masalimo 67 - Buku LopatulikaAmitundu alemekeze Mulungu Kwa Mkulu wa Nyimbo, pa Neginoto. Salimo. Nyimbo. 1 Atichitire chifundo Mulungu, ndi kutidalitsa, atiwalitsire nkhope yake; 2 kuti njira yanu idziwike padziko lapansi, chipulumutso chanu mwa amitundu onse. 3 Anthu akuyamikeni, Mulungu; anthu onse akuyamikeni. 4 Anthu akondwere, nafuule mokondwera; pakuti mudzaweruza anthu molunjika, ndipo mudzalangiza anthu padziko lapansi. 5 Anthu akuyamikeni, Mulungu; anthu onse akuyamikeni. 6 Dziko lapansi lapereka zipatso zake, Mulungu, Mulungu wathu adzatidalitsa. 7 Mulungu adzatidalitsa; ndipo malekezero onse a dziko lapansi adzamuopa Iye. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi