Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 67:2 - Buku Lopatulika

2 kuti njira yanu idziwike padziko lapansi, chipulumutso chanu mwa amitundu onse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 kuti njira yanu idziwike pa dziko lapansi, chipulumutso chanu mwa amitundu onse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Njira yanu idziŵike pa dziko lonse lapansi, chipulumutso chanu chidziŵike pakati pa mitundu yonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Kuti njira zanu zidziwike pa dziko lapansi, chipulumutso chanu pakati pa mitundu yonse.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 67:2
19 Mawu Ofanana  

Pakuti chifundo chake cha pa ife ndi chachikulu; ndi choonadi cha Yehova nchosatha. Aleluya.


Mwapatsa chimwemwe mumtima mwanga, chakuposa chao m'nyengo yakuchuluka dzinthu zao ndi vinyo wao.


Adani anga andinenera choipa, ndi kuti, adzafa liti, ndi kutayika dzina lake?


Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu: pakuti ndidzamyamikanso, ndiye chipulumutso cha nkhope yanga, ndi Mulungu wanga.


inde, ati, Chili chinthu chopepuka ndithu kuti Iwe ukhale mtumiki wanga wakuutsa mafuko a Yakobo, ndi kubwezera osungika a Israele; ndidzakupatsanso ukhale kuunika kwa amitundu, kuti ukhale chipulumutso changa mpaka ku malekezero a dziko lapansi.


Yehova wavula mkono wake woyera pamaso pa amitundu onse; ndi malekezero onse a dziko lapansi adzaona chipulumutso cha Mulungu wathu.


Ndipo tsopano, Mulungu wathu, mumvere pemphero la mtumiki wanu, ndi mapembedzero ake, nimuwalitse nkhope yanu pamalo anu opatulika amene ali opasuka, chifukwa cha Ambuye.


Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera:


ndipo anthu onse adzaona chipulumutso cha Mulungu.


nati, Wodzala ndi chinyengo chonse ndi chenjerero lonse, iwe, mwana wa mdierekezi, mdani wa chilungamo chonse, kodi sudzaleka kuipsa njira zolunjika za Ambuye?


Iyeyo anaphunzitsidwa m'njira ya Ambuye; pokhala nao mzimu wachangu, ananena ndi kuphunzitsa mosamalira zinthu za Yesu, ndiye wodziwa ubatizo wa Yohane wokha;


ndipo ndinalondalonda Njira iyi kufikira imfa, ndi kumanga ndi kupereka kundende amuna ndi akazi.


Pamenepo ndipo Mpingo wa mu Yudeya yense ndi Galileya ndi Samariya unali nao mtendere, nukhazikika; ndipo unayenda m'kuopa kwa Ambuye ndi m'chitonthozo cha Mzimu Woyera, nuchuluka.


Pakuti chaonekera chisomo cha Mulungu chakupulumutsa anthu onse,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa