Masalimo 26 - Buku LopatulikaDavide popempha Mulungu amweruze, atchula zokoma zake Salimo la Davide. 1 Mundiweruze, Yehova, pakuti ndayenda mu ungwiro wanga, ndipo ndakhulupirira Yehova, sindadzaterereka. 2 Mundiyesere, Yehova, ndipo mundisunthe; yeretsani impso zanga ndi mtima wanga. 3 Pakuti chifundo chanu chili pamaso panga; ndipo ndayenda m'choona chanu. 4 Sindinakhala pansi ndi anthu achabe; kapena kutsagana nao anthu othyasika. 5 Ndidana nao msonkhano wa ochimwa, ndipo sindidzakhala nao pansi ochita zoipa. 6 Ndidzasamba manja anga mosalakwa; kuti ndizungulire guwa la nsembe lanu, Yehova; 7 kuti ndimveketse mau a chiyamiko, ndi kulalikira ntchito zanu zonse zozizwa. 8 Yehova, ndikonda chikhalidwe cha nyumba yanu, ndi malo akukhalamo ulemerero wanu. 9 Musandichotsere mzimu wanga pamodzi ndi olakwa, kapena moyo wanga pamodzi ndi anthu okhetsa mwazi; 10 amene m'manja mwao muli mphulupulu, ndi dzanja lao lamanja ladzala ndi zokometsera mlandu. 11 Koma ine, ndidzayenda mu ungwiro wanga; mundiombole, ndipo ndichitireni chifundo. 12 Phazi langa liponda pachidikha, m'misonkhano ndidzalemekeza Yehova. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi