Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 26:11 - Buku Lopatulika

11 Koma ine, ndidzayenda mu ungwiro wanga; mundiombole, ndipo ndichitireni chifundo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Koma ine, ndidzayenda m'ungwiro wanga; mundiombole, ndipo ndichitireni chifundo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Koma ine ndimayenda mokhulupirika, mundikomere mtima ndipo mundipulumutse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Koma ine ndimakhala moyo wosalakwa; mu msonkhano wa anthu anu ndidzatamanda Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 26:11
19 Mawu Ofanana  

Mundikumbukire Mulungu wanga mwa ichi, nimusafafanize zokoma zanga ndinazichitira nyumba ya Mulungu wanga, ndi maudikiro ake.


Ndipo ndinauza Alevi kuti adziyeretse, nabwere, nasunge pazipata kupatula tsiku la Sabata. Mundikumbukire ichinso, Mulungu wanga, ndi kundileka monga mwa chifundo chanu chachikulu.


ndi chopereka cha nkhuni pa nthawi zoikika, ndi wa zipatso zoyamba. Mundikumbukire, Mulungu wanga, chindikomere.


Koma akazembe akale ndisanakhale ine, analemetsa anthu, nadzitengera kwa iwo mkate, ndi vinyo, pamodzi ndi siliva masekeli makumi anai; angakhale anyamata ao anachita ufumu pa anthu; koma sindinatero ine, chifukwa cha kuopa Mulungu.


Panali munthu m'dziko la Uzi, dzina lake ndiye Yobu; ndipo munthuyu anali wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu ndi kupewa zoipa.


Ndidzachita mwanzeru m'njira yangwiro; mudzandidzera liti? Ndidzayenda m'nyumba mwanu ndi mtima wangwiro.


Mundiweruze, Yehova, pakuti ndayenda mu ungwiro wanga, ndipo ndakhulupirira Yehova, sindadzaterereka.


Koma Mulungu adzaombola moyo wanga kumphamvu ya manda. Pakuti adzandilandira ine.


kuombola mbale sangadzamuombole, kapena kumperekera dipo kwa Mulungu.


Yandikizani moyo wanga, ndi kuuombola; ndipulumutseni chifukwa cha adani anga.


Kumbukiranitu tsopano, Yehova, kuti ndayenda pamaso panu m'zoonadi ndi mtima wangwiro, ndipo ndachita zabwino pamaso panu. Ndipo Hezekiya analira kolimba.


Ndipo onse awiri anali olungama mtima pamaso pa Mulungu, namayendabe m'malamulo onse ndi zoikika za Ambuye osachimwa.


Inu ndinu mboni, Mulungunso, kuti tinakhala oyera mtima ndi olungama ndi osalakwa kwa inu akukhulupirira;


amene anadzipereka yekha m'malo mwa ife, kuti akatiombole ife kuzoipa zonse, nakadziyeretsere yekha anthu akhale ake enieni, achangu pa ntchito zokoma.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa