Masalimo 61 - Buku LopatulikaPoopsedwa Davide athamangira Mulungu Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Neginoto. Salimo la Davide. 1 Imvani mfuu wanga, Mulungu; mverani pemphero langa. 2 Ku malekezero a dziko lapansi ndidzafuulira kwa Inu, pomizika mtima wanga. Nditsogolereni kuthanthwe londiposa ine m'kutalika kwake. 3 Pakuti munakhala pothawirapo panga; nsanja yolimba pothawa mdani ine. 4 Ndidzagoneragonerabe m'chihema mwanu; ndidzathawira mobisalamo m'mapiko anu. 5 Pakuti Inu, Mulungu, mudamva zowinda zanga; munandipatsa cholowa cha iwo akuopa dzina lanu. 6 Mudzatalikitsa moyo wa mfumu. Zaka zake zidzafikira mibadwomibadwo. 7 Adzakhala nthawi zonse pamaso pa Mulungu; mumpatse chifundo ndi choonadi zimsunge. 8 Potero ndidzaimba zolemekeza dzina lanu kunthawi zonse, kuti ndichite zowinda zanga tsiku ndi tsiku. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi